Mtsikana wadziphera m’nyumba ya bwenzi lake

Advertisement
Suicide

Mtsikana wa zaka 17 wadzipha podzimangilira ndi neti yozitetezera ku udzudzu m’nyumba ya chibwezi chake pomwe amachokera ku sukulu ya sekondale ya Mphande m’boma la Mwanza.

Malingana ndi ofalitsa nkhani pa polisi ya Mwanza Sergeant Hope Kasakula, mtsikanayu yemwe wazindikilidwa ngati Kithuwe Mtunduwatha wapanga izi sabata yatha pa 25 October, 2023 m’mudzi mwa Mchotseni, m’dera la Mfumu Kanduku Maseko m’bomalo.

Apolisi ati monga mwa nthawi zonse, malemu Mtunduwatha patsikuli anadutsira kaye kunyumba kwa chibwenzi chakecho pomwe amapita ku sukulu ndicholinga choti akamuphikire kaye chakudya bwezi lakelo ndipo patsikuli mamunayo anadabwa kuti nyenyezi yakeyo imawoneka yosasangala kwenikweni.

A Kasakula anapitiliza kufotokoza kuti Mtunduwatha ataweluka kusukulu, adayimanso kunyumba kwa chibwezi chakecho koma pa nthawiyi mamunayo anali atapita kumaganyu kukasaka chakudya cha madzulo a tsiku limenelo.

Mneneri wa polisiyu wati madzulo atsikulo atabwerako kumaganyuko, mnyamatayo adapeza chitseko cha nyumba yakeyo chili chotseka ndipo pomwe anatsekula ndi mphamvu adawona thupi la chibwenzi chakecho likulendewera kudenga kwa nyumbayo.

Nkhaniyi itakasiyidwa ku polisi ya Mwanza, apolisi ena ogwira ntchito ku nthambi yofufuza milandu ya Criminal Investigation Department (CID), adathamangira ku maloko ndi kutenga thupi la Mtunduwatha kupita nalo ku chipatala cha m’boma la Mwanza kuti akalipime.

Pakadali pano zotsatira za ku chipatalako ziwonetsa kuti msungwanayo adamwalira chifukwa chobanika pambuyo pa kupotokoledwa kwa khosi.

Advertisement