“Ndikubwera ku Malawi-ko kudzapha anthu oyipa” – watelo JB

Advertisement
Jolly Bro Malawian musician based in the United States

…wati nduna zachimuna zambiri ndi “zigandanga”

Oyimba Jolly Bro yemwe ali m’dziko la America, waopseza kuti abwera ku Malawi kuno chaka cha mawa kudzathana ndi nduna zina zomwe akuti ndi zoyipa kuphatikizaso anthu omwe anapha Allan Wittika.

Izi ndi malingana ndi kanema yemwe Alberto Fernando Zacharias otchedwaso JB anajambula layivi (live) pa tsamba lake la fesibuku lachiwiri sabata ino momwe amakamba zambiri zokhudza kuphedwa kwa Allan Wittika mwezi watha munzinda wa Lilongwe.

Mukanemayi, JB anati ndiodabwa kuti munthu amene akuganizilidwa kuti anapha Wittika a Lester Maganga omweso ndi othandizira nduna yofalitsa nkhani Moses Kunkuyu, atachita chipongwechi anapita ku South bend m’dziko la America komwe akuti kumakhalaso nkulu wake wa malemuyu yemwe dzina lake akuti ndi Dingaan.

“Ineyo chandibhowa nchakuti Lester Maganga yemwe anapha Allan Wittika anabwera kuno ku South bend (America) komwe kuli mkulu wake wa Wittika-yo, Dingaan. Nde iyeyo amabwera kuno kudzatani? Kapena amafuna adzapheso mkulu wa Allan-yo? Kapena amafuna kudzalimbana ndi JB?” anatelo JB.

Oyimbayu anapitilira ndikudzudzula nduna zina zomwe akuti zikuzuza a Malawi komaso zikukhudzidwa ndi imfa ya Wittika ndipo wati nkwabwino kuti pano azimayi adziyikidwa mmaudindo apamwamba ponena kuti azimayi sangachite zoyipa zomwe nduna zina zachizibambo zikupanga.

“Zikhale Ng’oma ndi munthu oti mungamuvotele kuti akhale nduna? Moses Kunkuyu? Kumawona anthu owavotera, mukuvoteratu zimbava, zigandanga zi anthu zakupha. Kuyambira lero tiyeni tidzivotera azimayiwa chifukwa azimayiwa sangapange izizi, azimayi sangamuwombele munthu nkamwa.

“Ine simumandidziwatu, ka Kunkuyu-ko ine nditati ndafuna nditha kukasakasaka kukapeza ndikukapha. Ka Maganga-ko nkanakhala kuti ndadziwa kuti kanali ku South bend kunoku kanakabwelera ntembo ku Malawi-ko. M’bale wake wa Allan Wittika ndalira naye panjapa ineyo ma week apitawo, tinakadziwa kuti Lester Maganga anali ku South bend konkuno tinakamupha ameneyo,” anateloso Jolly Bro.

Kamba kopsa mtima ndi zomwe akuti zikuchitika m’dziko muno, oyimbayu yemwe amazijambura mfuti ili m’manja, wati akulingalira zoti abwere chaka cha mawa kudzathana ndi aliyese yemwe akuzuza anthu kuphatikizapo onse omwe akuganizilidwa kuti anapha Wittika.

“Ife sitimasewera choncho ayi. Simungamawaopseze anthu ku Malawi-ko? A Zikhale Ng’oma ine simungandiopseze, mwachepa. Ine ndimfana owopsa, ine ndi mvyete, ndikuphani nose anthu oyipa. Inu mungamazuze anthu omweso anakuvoterani, iwo kumakhala akapolo anuso?

“Ine ndibweratu kumeneko chaka cha mawa basi ndidzangoyambitsa nkhondotu, mukuona bwanji a Malawi? Tingopha onsewa. Ine sindimanyengelera, nde muuzane kumeneko kuti mukamapanga masewera kumaona ngati mafana apa Malawi ndiogona, ife siogonatu,” anawonjezeraso choncho JB.

Asanajambule kanemayi, JB kudzera patsamba lake la fesibuku, anadzudzulaso nduna ya zachitetezo a Zikhale Ng’oma kuti akulephera bwanji kutseka kampani ya zachitetezo ya a Kunkuyu monga momwe anachitira ndi kampani ya Ichocho.

“Zikhale Ng’oma sukutseka security company ya kunkuyu ngati m’mene unapangila ya ichocho ija bwanji? Ichocho sanalakwe kanthu koma mudamutsekela sichoncho? Ndipo iweyo umakonda kutiophyeza anthufe tikapanga raise ma concerns chifukwa chani? Tizikuopa iweyo ndi tianzakoto?? Iwetu iwe!!! Usamale!” Walemba choncho JB pa tsamba lake la fesibuku.

Advertisement