Boma lati ndalama zokwana K800 miliyoni ziperekedwa ku ntchito yomangira mabwalo amasewero a FCB Nyasa Bullets ndi Mighty Mukuru Wanderers.
Nduna ya zamasewero Uchizi Mkandawire ndi yomwe yanena izi lero.
Malingana ndi a Mkandawire, ntchitoyi inaima m’mbuyomu kamba ka ngongole zina zomwe makontilakitara a mabwalowa anali nazo komanso kukwera mitengo kwa zipangizo zina zogwilira ntchitoyi.
Nkhani yomanga mabwalo a masewero a matimu a Bullets ndi Wanderers inayamba nthawi ya ulamuliro wa a Peter Mutharika ndi Democratic Progressive Party (DPP) mu nthawi ya kampeni pomwe zinkayandikira zisankho za 2019.
A Lazarus Chakwera atasankhidwa kukhala mtsogoleri wa dziko lino, nduna yawo yoyamba ya zamasewero a Ulemu Nsungama anauza nyumba zofalitsa kuti ntchito yomanga mabwalowa sinali mu mapulani a boma la a Chakwera.