Chilima: Munthu wanzeru saotcha tchire nyumba ilibe chimbudzi

Advertisement

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima ati munthu wa nzeru saotcha tchire lozungulira nyumba ngati nyumbayo ilibe chimbudzi.

Iwo ananena izi dzulo ku Kamuzu International Airport poyankhula ndi owatsatira pomwe amafika mdziko muno kuchokera ku United States of America.

Iwo anapereka miyambi iwiri ndipo oyamba ndi okuti okazinga soya sadikira mbuliuli pomwe wachiwiri ndi okuti munthu wa nzeru saotcha tchire lozungulira nyumba ngat aline chimbudzi.

A Chilima anakana kupereka tanthauzo la miyambiyi ponena kuti nthawi yatha koma anauza owatsatira kuti atanthauzire okha.

Miyambiyi a Chilima anena pomwe zikumveka kuti pali kusagwirizana pakati pa iwo ndi a mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera.

Amalawi ena pa Fesibuku akuti miyambiyi ikusonyeza kuti pali nkhani yaikulu yomwe itamveke kutsogoloku. Koma ena akuti a Chilima amangocheza ndi owatsatira.

Komabe enanso ati miyambiyi singathandize kuwachotsa a Malawi mu mavuto omwe akukumana nayo. Iwo apempha a Chilima kuti chidwi chawo chikhale pa ntchito yotukula a Malawi.

Ali ku United States, a Chilima anauza a Malawi okhala kumeneko kuti ubale wa pakati pa atsogoleri awiriwa komanso zipani zawo uli bwino.

 

Advertisement