Shadric Namalomba wati anthu asiye kulubwalubwa za umoyo wa m’tsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika ponena kuti aMalawi adamusankha okha atamukonda posayang’anira zaka zake chonsecho achinyamata oti nkuwavotera adalipo.
Namalomba yemwe ndi nduna ya zofalitsa nkhani komanso woyankhulira boma, wayankhula izi Lachisanu pomwe amayankhula ndi wailesi ya Zodiak.
Kuyankhulaku kukudza pomwe anthu ochuluka akudzudzula boma kuti silikubwera poyera ndikufotokoza bwino za umoyo wa a Mutharika pomwe akhala nthawi yaitali osawonekera ku gulu.
Mwachitsanzo, bungwe la Public Affairs Committee (PAC) lidati chete wa boma pa kusawoneka kwa a Mutharika ali ndikuthekera kokakamiza anthu kumafalitsa nkhani zabodza monga zakhala zikumvekera kuti m’tsogoleriyu wadwalika.
PAC yati ikufuna a Mutharika atuluke ndikuyankhula ku mtundu wa a Malawi pompopompo (live) osati mauthenga ongojambula monga zakhala zikuchitikira pakatipa.
Komatu a Namalomba akana mwantu wagalu mphekesera yoti a Mutharika adwalika ponena kuti m’tsogoleriyu ali nganganga ndipo palibe pomwe pakumutsinatsina.
Komabe, Namalomba wati anthu akuyenera kuwamvetsetsa a Mutharikabmmene aliri.
“Purezidenti Mutharika ayenera kumvetsetsedwa potengera udindo wake monga Mtsogoleri wa dziko, osati kumuyerekezera ndi nduna, phungu wa Nyumba ya Malamulo kapena councillor,” water Namalomba.
Kuwonjezera apo, ndunayi yati anthu sakuyenera kuyankhulitsa ponena kuti adawasankha a Mutharika pa chisankho cha chaka chatha akudziwa kale kuti ndi a akulu.
“Pa pepala la chisankho panali achinyamata, koma a Malawi anasankha Mutharika. Amamukonda mmene alili, choncho anthu asiye kufalitsa nkhani zabodza zokhudza umoyo wake. Iye sakudwala,” adatero Namalomba.
Apa ndipomwe Namalomba adatsindika kuti Mutharika akugwira ntchito yake bwino bwino, osati monga anthu akufalitsira kuti wadwalika zedi.