Khansala wa chipani cha MCP ku wadi ya Mbongozi, kumpoto chakum’mawa kwa boma la Kasungu, Charles Zaipa Binya, wasankhidwa kukhala wapampando wakhonsolo ya bomali.
Binya wapambana pa zisankho zomwe zinachitika Lachinayi pa 26 November, 2026 pamkumano wa khonsoloyi, ndipo a Shilla Nkhata achipani cha MCP a wadi ya Misozi ndiye wachiwiri wawo.
Anthu ena omwe anaonetsa chidwi pa pampandowu ndi a Fresha Nyirongo aku Milenje wodi komanso a Josephy Banda aku N’thabuwa Wodi.
Apa a Binya alowa m’malo mwa a Khansala Nephtali Chikwanda a wadi ya Chipala pamene a Nkhata alowa m’malo mwa a Teleza Kanyukuta a wodi ya Chibophi.
Bwanamkubwa wa bomali a Lawford Palani ati ndiwosangalala monga mwa lamalo kuchokera kuunduna wa maboma ang’ono kuti khonsolo zizisankha adindo atsopano pakatha chaka ndipo ati akuyembekezera kuti utsogoleri wa tsopanowu uyika patsogolo zosowa za anthu pa nkhani ya zitukuko.
Poyankhulapo a Binya anati anthu ayembekezere kuti iwo agwira ntchito moyikapo mtima ndipo awonetsetsa kuti zitukuko zonse zomwe zili pansi pa thumba la CDF zikugwilidwa molongosoka.








