Msewu wa Mbeta uthilidwa phula


Mseu- Malawi24

Chiyembekezo ndi chimwemwe zakula pakati pa anthu maka ochita malonda ku Kasungu pomwe Manisipalite yawo yalengeza kuti mwezi ukudzawu, iyamba ntchito yothira phula msewu wa Mbeta.

Msewu wa Mbeta ndiomwe umachokera pa Nation Bank kudutsa pa St Joseph kukatulukira mu msewu wa M1 ndipo kupatula kuika phula uyikidwaso magetsi amumsewu oyendera mphamvu yadzuwa .

Mfunu ya Manisipalite ya Kasungu a Hasting Nyirongo ndiyo atsimikiza za nkkhaniyi poyankhulana ndi tsamba la Malawi24 ndipo wati ntchitoyi iyamba mwezi wa December’wu.

A Nyirongo ati manisipaliteyi ikozanso mlatho wa Mbeta omwe ukhale wamakono ndikuyika ma magetsi a munsewu oyendera dzuwa.

Iwo ati ntchitoyi igwilika ndi ndalama zokwana K3,727, 012, 366 kuchokera Ku Roads Fund Administration (RFA) ndipo igwilika kwa miyez isanu komanso ikuyembekezeka kudzatha mmwezi wa May 2027.

Damiano Linkoni Ochita Malonda- Malawi24
Linkoni

A Owen Nkhoma omwe amayendetsa galimoto za matola ati akuyamika Manisipalite ya Kasungu kaamba kaganizoli ponena kuti zichepeza mavuto omwe amakumana nawo maka munyengo ya mvula.

“Munthawi ya mvula timakhala pamavuto akulu zedi chifukwa cha matope a mnsewu umenewu kotero ndine osangalala kuti mseu umenewu akuyika phula,” Nkhoma.

Nawo a Damiano Linkoni am’mudzi mwa a. Gundani omwe ndi ochita malonda ati ntchitoyi ithandiza kuti anthu apeze ntchito zomwe zichepetse ulova omwe wakula.

Latest vacancies

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading