Amayi akhale patsogolo kupemphelera dziko, zisankho – Kwelepeta

Advertisement
Women's Day of Prayer - Zomba

Phungu wa dela la Zomba Malosa, Grace Kwelepeta walimbikitsa amayi kuti akhale patsogolo kuyamika komanso kupemphelera dziko maka pamene dziko la Malawi likuyandikira kupita ku masankho ponena kuti mapemphelo ndi omwe amabweletsa umodzi ndi kupeleka atsogoleri oyenera komanso kupulumutsa dziko ku zophinja.

A Kwelepeta anayankhula izi pomwe anakhala nawo pa mwambo wa mapemphero wa amayi omwe anachitikira pa bwalo la Domasi m’boma la Zomba. A Kwelepeta anati mapemphero anapulumutsa dziko la Malawi ku ngozi zoopsa zogwa mwadzidzidzi zomwe zinagunda ma dera ena koma dera lawo kunali chiwelengelo chochepa cha okhudzidwa.

Phunguyu anati mphamvu ya mapemphero imapeputsa ntchito yomwe atsogoleri amakhala nayo pa anthu awo maka mulungu akapulumutsa dera ku ziphinjo monga zinalili ndi mphepo ya mphamvu ya Jude ndi ngozi zina.

“Kukagwa ngozi zadzidzidzi kwambiri zimakhudza mtsogoleri, ndipo kupanda kuyika mulungu patsogolo ndekuti sungapulumuke ku ngozi ngati izi. Mulungu amayenera ayikepo dzaja pa utsogoleri kotero kumafunika kukhala pamodzi moyanjana ndi kuyamika, ndipo ine ngati mtsogoleri wawo ndimayenera nditsogolere kuwonetsa umodzi m’mapemphero,” Kwelepeta anafotokoza.

Mlendo olemelezeka pa mwambowu Maggie Kathewera Banda, yemwenso ndi mkulu wa bungwe la Women’s Legal Resource Centre (Worlec) anati mzimayi ndi munthu ofunika ndipo kulimbikitsana ndi kofunika komanso kukumbutsana kuti amayi azindikire kuti ali ndi kuthekera pochita zinthu mdziko ngakhale pakhomo pawo pomwe.

A Kathewera Banda anati monga mwa mutu wa mapemphero a lero, kumakhala kofunika kuti amayi asiye zonse zowalekanitsa ngati amayi mu dera ndi kubwera pamodzi kudzapeza mayankho pa zovutazo, komanso kudzazindikira kuti ali ndi ntchito ndi udindo ochitapo kanthu mu gawo lililonse mdziko.

Wapampando wa mapempherowa mayi Ivy Wilson Mponda ati chaka chilichonse kumakhala mapemphero , koma kunali kofunika kuti iwo ngati amayi asakhalebe chete mukupemphera makamaka kupempha mulungu kuti apeleke atsogoleri oyenera owopa mulungu kuti atumikire anthu m’dera ndi mdziko la Malawi pamene Malawi akupita ku masankho.

“Mzimayi ndi ofunika pa zinthu ndipo ndife odala chifukwa chokhala ndi phungu wa chizimayi, tinawayitana dala kuti tiwonetse kuti amayi tili ndi udindo waukulu kwambiri,” anafotokoza a Mponda.

Amayi a madera a Songani, Domasi komanso Malosa, atatha kupanga mapemphero a pawokha-pawokha masabata apitawo, lero ndi pomwe anabwera pamodzi kupanganso mapemphero kulimbikitsa umodzi monga mwa mmene akhala akuchitira zaka zonse.

Kumapemphelowa kunawelengedwa mawu molandirana, ndi kuwelenga ndime za m’buku lopatulika molandirana ndipo amachitika pa mutu oti “Tipatseni dziko lathu lathu” kuchokerapa Numeri 27 ndime ya 4, ndipo mapempherowa anayitana amayi ochokera ku mipingo ya chikhristu ndi a chipembedzo cha chisilamu pomwenso panafika oyimba nyimbo za uzimu monga Phalyse Mang’anda, Favoured Martha mwa ena.