
Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera wati ululu wa kukwera kwa mitengo ya zinthu mdziko lino bwezi uli owonjeza pakadapanda alimi a fodya pomwe wati otsutsa akanalimbikitsa ulimi wafodya osati ziwonetselo bwezi Malawi atapita patali.
Pakali pano, mtengo okwera wagona pa $3.2 ndipo $1.2 otsikitsitsa.
Poyankhula pa mwambo otsekulira msika wa fodya ku Kanengo mu mzinda wa Lilongwe, a Chakwera ati ngongole za katapira zomwe maboma ambuyomo adatenga zidaputira dziko lino mavuto, pomwe ati zomwe zuthandiza kwambiri ndi ulimi maka wa fodya
Iwo ati chilowere m’boma akhala akulongosola za ngongole zomwe ena anatenga m’buyomu ndipo ati zikadakhala kuti ndondomeko za minda ya ikulu ikulu zidayamba 1994 bwezi chuma cha Malawi chili patali.
“Olo lero akanakhala kuti zipani zotsutsa boma zikulimbikitsa mlimi wafodya, koposa kulimbikitsa ma demo bwezi chuma chathu chili potani?, nthawi zina izi timalimbikitsa zimakhala zomvetsa chisoni,” anatero a Chakwera
Iwo awonjezera kuti saleka kupititsa chitukuko cha fodya patsogolo, chifukwa ubale wa iwo ndi mlimi wa fodya ndi weniweni.
Mtsogoleri wa dzikoyu wati popanda alimi a fodya dziko lino likanavutika chifukwa ndalama za kunja zomwe dziko linapeza zinakwanitsa kugula chimanga kunja kwa dziko lino ndi kupulumutsa miyoyo ya anthu ochuluka omwe anakhudzidwa ndi ng’amba.
“Popanda inu alimi a fodya ululu omwe tikuumva mdziko muno kamba ka ng’amba yomwe yawononga minda yambiri bwezi titafika pa ululu wa dzaoneni, koma ululuwu tikuuzizilitsa ndi chimanga chomwe tinayamba kugawa chaka chatha chomwe chinapezeka chifukwa cha Forex kudzera mwa mlimi wa Fodya,” anatelo a Chakwera.
Msika wafodya unasokonekera lero pomwe alimi ena anadandaula za mitengo yomwe ogula akupeleka ponena kuti ndi yochepa kwambiri, pomwe ati fodya wambiri amagulidwa $1 pa kilo zomwe anati kulibwino akagulitse kwina.
A Memory Chikuwi omwe ndi mlimi anati mitengo pakadali pano siyabwino chifukwa sizikugwirizana ndi zolowetsa m’minda yawo komanso poganizira ngongole yomwe adatenga ku NEEF kuchitira ulimi.
Nduna ya za ulimi a Sam Kawale ayamika alimi a fodya chifukwa cha fodya wapamwamba yemwe alimi akubweretsa, zomwe zakondweletsa ogula ndi unduna.
Wapampando wa Tobacco Commission, Godfrey Chapola wati ogula anawonetsa chidwi chogula 200 million kilograms koma dziko lino likolola 170 million kilograms zomwe zikweze mtengo komanso ndi mkokomkoke pa msika wa fodya.
Pomwe msika wa Kanengo awutsekulira, msika wa Chinkhoma ku Kasungu, Limbe ku Blantyre ndi Mzuzu akhale akutsekuliranso mwezi omweuno pomwe ati ma belo oposa 35, 000 adzikhala akugulidwa pa tsiku.
Uyu atitukwanitsa🙄