
…Ekhaya yagona pamwamba itadya Tigers…
Akatswiri a 2024 TNM Super League, Silver Strikers lero ayamba udyo mu masewelo awo otsekulira masewelo a chaka chino cha 2025 TNM Super League pomwe agonja 1-0 ndi FCB Nyasa Big Bullets pa bwalo la Bingu mu mzinda wa Lilongwe.
Chigoli cha Babatunde Adepoju pa phindi ya chi 29 atalandira mpira kuchokera kwa Wongani Lungu ndi chomwe chayambitsa Silver Strikers udyo ulendo, pomwe chigawo chonse choyamba osewera a Mgangira amasewera ngati opanda cholinga.
Silver inayamba masewelowa ndi osewela monga; George Chikooka, Macdonald Lameck, Maxwell Paipi, Shema,Sambani Kamanga, Chimwemwe Idana, Uchizi Vunga, Chinsinsi Maonga, Zebron Kalima ndi Binwell Katinji pomwe FCB Nyasa Big Bullets inayamba ndi Richard Chimbamba, Yamikani Mologeni, Joseph Mpokera, Salima Singo, Babatunde , Wongani Lungu, Phodo Jovinala ndi Lloyd Aaron.
Silver inayesa kusintha kangapo konse koma kumbuyo kwa anyamata a ku Blantyre kumakanika kudutsika ngakhale pa mphindi ya chi 68 McDonald Lameck anaphonya pang’onong’ono atalandira mpira kuchokera kwa Duwe ndi Sandukira atapatsilana mwapamwamba.
Bullets inapata chigoli chachiwiri kudzera mwa Maxwell Phodo pa mphindi ya chi 51 koma othandizira oyimbira, Easter Zimba anayimika mbendera kuti Phodo analawira mbali ya weni zomwe ambiri atsutsapo.
Mphunzitsi was Silver, Peter Mgangira wati kugonja kwa lero simathero a zonse potengera kuti ligi yangoyamba ndipo wati sanasewele bwino m’gawo loyamba koma watsindika kuti akonza mavuto omwe wawawona.
Mphunzitsi wa Bullets Peter Mponda yemwe wangochoka ku Silver Strikers wati ndi oyamika ndipo anati iwo amayenera kupambana basi.
Masewelo ena otsekulira ligi lero timu yomwe yangolowa kumene ya Ekhaya lero igona pamwamba pomwe yaswa a mkhalakale a Mighty Tigers 2-0 pa bwalo la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre ndi zigoli za Lovemore Mbeta pa mphindi ya chi 40 ndi Emmanuel Saviel pa mphindi ya 90.
MAFCO yadya Chitipa United 1-0 ndi zigoli za Yohane Malunga kuti usiku uno asilikali agone pa nambala 3 pa mndandanda.
Mndandanda wa lero Ekhaya ndi yomwe ikutsogolera kenako Bullets kutsatira MAFCO pomwe onse atola ma points atatu-atatu mu mpikisano wa TNM Super League sabata yoyamba.