
Kunali chipwilikiti ku Nyumba ya Malamulo kum’mawaku lero pomwe ena mwa anamandwa opanga malamulowa amafuna kuponyerana zibonyongo.
Chatsitsa dzaye nchakuti pomwe Madalitso Kazombo, wachiwiri kwa sipikala wa nyumba ya malamuloyi analengeza kuti oyimilira aMalawi-wa akatchaye kaye mtentha ndebvu, Patricia Kainga Nangozo anathera mawu aphungu ambali yotsutsa boma.
Kainga Nangozo yemwenso ndi wachiwiri kwa nduna yoona zaubale wa dziko lino ndi mayiko ena, anachoka pomwe anakhala ndikupita kukathera zakukhosi phungu wa dera la Blantyre City South East, Sameer Suleman. Sonthoo! Mtima wa Suleman unanyamuka mpaka kufuna kumuwonetsa Chitsulo kuti washosha mavu nkhomola.
Zinatengera aphungu ambali zonse ziwiri kulowelera kuti opanga malamula asalawule dziko ndi nkhani yoti awonetsana nyenyezi.