Nyumba za Adam zikunyasitsa mzinda wa Zomba – zatero mzika zokhudzidwa

Advertisement
H Adam

Mzika zina zokhuzidwa zaloza chala m’mwenye ochita malonda a H Adam kuti nyumba zake zikunyatsitsa mzinda wa Zomba popeza ndizosawoneka bwino.

Patrick Gama yemwe amachita bizinesi yokonza foni zowonongeka wati pali nyumba zina zomwe zili m’phepete mwa ssewu waukulu ochokera ku Blantyre kupita ku Lilongwe ndizofunika kuzigwetsa ndikumanga zina chifukwa zikunyatsitsa mzinda wa Zomba.

Iye adapereka chitsanzo cha nyumba ina yomwe ili m’phepete mwa nsewu wa Blantyre moyang’anizana ndi Parishi ya St George’s Anglican yomwe mwini wake ndi m’mwenyeyu wati ndiyofunika kuti igwetsedwe ndikumanga ina popeza ndiyosawoneka bwino

Gama adapempha akulu akulu a khonsolo ya mzinda wa Zomba kuti achitepo kanthu mwansanga popereka chenjezo kwa eni ake anyumbazi ndipo adapemphanso unduna wa maboma ang’ono kuti ulowelerepo.

“Tipemphe khonsolo ya mzinda wa Zomba kuti asamangolekelera anzathu akhungu lachimwenye kuti aziwononga mzinda wathu nawonso amange momwe akuchitira anthu okuda omwe akumanga mwamakono nyumba zawo mumzinda uno,” iwo adatero.

Ndipo a Francis Tambala omwe ndi m’phunzitsi wa pulayimale adati akumva chisoni powona momwe mzinda wa Zomba ukuwonekera ndipo ukusiyana kwambiri ndi mizinda ina yonse potengeranso kuti ndi likulu la dziko loyambilira kuno ku Malawi.

Iye adati nyumba ya H Adam komanso nyumba ya Chipiku Wholesalers zikuyenera kuti ziyikidwe chizindikiro chamtanda wofiyira pofuna kuti zigwetsedwe ndikumangidwapo zina zamakono zomwe zipangitse kuti mzindawu uziwoneka bwino.

Pamenepa Tambala adapereka chitsanzo cha mtsogoleri wadziko lino pazomwe adayankhula kumtundu wa a Malawi panthawi yomwe amatsekulira nyumba ya malamulo kuti akufuna kuti pofika chaka cha 2030 Mzinda wa Zomba udzakhale owoneka bwino komanso wamakono ndipo adati izi zikhoza kudzatheka ngati nyumba zina zitamangidwanso.

Koma poyankhapo madandaulowa, mkulu wa khonsolo ya Mzinda wa Zomba Archangel Bakolo adati zomwe akudandaula anthuwa ndizomveka.

Iwo adati khonsolo ya mzinda wa Zomba idalembera kale kalata eni nyumbazo kuti azigwetse ndikumanga zina.

A Bakolo ati adapereka malire kuti pofika pa 15 April 2025 mwezi wamawa eni nyumbazi akhale atawayankha makalata awo ndipo kupanda kutero khonsoloyi idzachitapo kanthu.