
Nduna ya zamalonda, Vitumbiko Mumba wanenetsa kuti salora m’dziko muno kuchitika malonda osatsatira malamulo chifukwa chothandiza chipani ndi ndalama ngati chiphaso chochitira malondawa.
Mwa zina, Mumba wanena kuti unduna wake uwonetsetsa kuti ochita malonda m’dziko muno akuchita malondawa motsata malamulo komaso mopindulira dziko lino.
Iye ananena kuti pali amwenye ambiri amene amachita malonda awo mozembera boma kupereka msonkho maka ogulitsa kaunjika.
Ndunayi inaonjezeraso kudzudzula mchitidwe wa sitolo zikuluzikulu zomwe zimagulitsa katundu ochokera kunja mwadala kusiya katundu opangidwa mu m’dziko muno.
Ndunayi imalankhura izi pa msonkhano wa atolankhani omwe unduna wawo unachititsa mu mzinda wa Lilongwe Lolemba.