
Apolisi m’dziko muno ati akwanitsa kumanga munthu m’modzi yemwe akumuganizira kuti akukhudzidwa nawo pa zipolowe zomwe akuluakulu ena komanso otsatila chipani cha Malawi Congress (MCP) anachitilidwa dzulo ku Nselema m’boma la Machinga.
Ofalitsa nkhani za apolisi m’dziko muno, a Peter Kalaya atsimikiza kuti pakadalipano amanga a Lanjesi Mkwanda a zaka 30 ochokera m’mudzi mwa Mwitiya, mfumu yaikulu Nyambi m’boma lomweri la Machinga.
A Kalaya ati pakadalipano apolisi alimbikitsa ntchito ya kafukufuku kuti agwile anthu ena omwe akukhudzidwa ndi zaupanduzi.
Iwo apitilizanso kulangiza anthu m’dziko muno kuti azipewa kugwilitsidwa ntchito ndi andale pochita zipolowe mu nyengo ino pamene dziko lino likuyandikira ku chisankho.
Komabe, anthu ambiri akuti akudabwa kwambiri ndi changu chimene apolisi apanga pofulumira kugwira oganizilidwa mu zipolowe za ku Machinga.
Mu mwezi wa February chaka chatha, otsatila chipani cha DPP adachitilidwa chiwembu pamene amayenda ulendo wa ndawala mu nzinda wa Lilongwe koma mpaka lero, tsogolo la nkhaniyi silikudziwikabe.