
Phungu wa Nyumba ya Malamulo ku dela la pakati m’boma la Thyolo a Ben Malunga Phiri, ati; Kodi kupeleka uthenga olakwika kwa mtsogoleri wa dziko kupitilira chonchi kufikira liti?
A Phiri ati pali anthu ena omwe atangwanika kupeleka uthenga onama okhudza zitukuko zina zomwe iwo adazitchula mu State of the Nation Address-SONA, ndipo a Phiri apeleka chitsanzo cha Bridging foundation.
Phunguyu wati SONA ndi chithu chofunika kwambiri nchifukwa chake anachiyika m’malamulo a dziko lino, ndipo kupeleka uthenga olakwika ndi kuwalakwira aMalawi.
Ku mathelo a sabata yapitayo katswiri pa ulamuliro wabwino ndi ndale, a Sheriff Kayisi potsilira mlomo pa SONA mu pologalamu ya ‘Contemporary issues” pa wayilesi ya Radio Islam adati anthu ena omuzungulira mtsogoleri wa dziko lino akumupatsa uthenga wabodza ndipo ati aka sikoyamba kuti mtsogoleri wa dziko apeleke uthenga wina omwe siowoona.
A Kayisi adatinso anthu omwe anapeleka uthenga wina omwe si owoona kwa mtsogoleri wadziko akuyenera kupeza zotsatira za kupeleka uthenga omwe si owona Kwa mtsogoleri wa dziko.