A Malawi valani zilimbe magetsi akwela ndi 16 pelesenti

Advertisement
Kumwenda

Pomwe a Malawi ambiri akukhala movutika malinga ndi kukwera kwa katundu nayo bungwe logulitsa magetsi la ESCOM laganiza zokweza  mtengo wa magetsi ndi 16 percent kuyambira lero.

Malinga ndi kalata  yomwe bungweli latulutsa, kukweraku cholinga chake nkufuna kuthandiza bwino makasitomala ake.

Kalatayi yati iyi ndi gawo lachiwiri lokweza magetsi mzaka zinayi lomwe bungwe lowona za mphamvu la MERA lidavomereza mu chaka cha 2023.

A Malawi ambiri adandaula ndi ganizoli chifukwa choti akudutsa kale mu nyengo zowawitsa.

Koma mkulu wa bungwe la ESCOM, a Kamkwamba Kumwenda ayikira kumbuyo ganizo lokweza magetsili, ndipo ati bungweli limayenera kukweza magetsi ndi 60 pelesenti koma Boma lawuza kuti akweze ndi 16 pelesenti.

“Magetsi amayenera kumakwera chaka ndi chako mu zaka zinayi potengera ndi m’mene zikukhalira m’dzikoli, maka kugwa kwa kwacha,’ iwo anatero.

Malinga ndi a Kamkwamba kwacha itagwa ndi 44 pelesenti mu 2023, magetsi adakwera ndi 16 pelesenti ku makasitomala a mafakitale mu chaka cha 2024.

“Izi zinachititsa kuti kampani yathu igwe mu ngongole yokwana K50b chifukwa choti timagula zipangizo, magetsi ku EGENCO komanso ku IPP pa mtengo wokwera koma timagulitsa motsika,”iwo anatero.