Gulu la amai la Sarah mu m’mpingo wa Living Waters International ku Bangula m’boma la Nsanje, lidakachezera odwala pa chipatala cha Kalemba mu nyengo yachikondwelero cha Khirisimisi.
Malingana ndi mai Mbusa Priscilla M’bwana, chimodzi mwa utumiki wa amai a Sarah ndikuyendera komanso kuchezetsa anthu odwala.
Iye ati m’chifukwa chake anachiona choyenera kudzasangalatsa odwala ku chipatalachi.
“Madalitso omwe Chauta atipatsa chaka chino ndibwino nafenso tiwafikire nawonso ena,” antero mai M’bwana.
Wachiwiri kwa mkulu pa chipatala cha Kalemba Rural Community Hospital Sister Moureen Chalamanda anathokoza amayiwa chifukwa chodzachezera odwala nyengo ino ya kubadwa kwa Ambuye Yesu.
Iye ati guluri lapereka mphatso kwa amai amene angobereka kumeneko mu chipinda chawo, amai ena akuyembekezera komanso kuchipanda cha amuna.
“Tili othokoza kwambiri pa zomwe gulu la amai a Sarah achita moti sitimayembekezera konse,” iwo anatero.
M’modzi mwa olandira Alinafe Zuze a zaka makumi awiri (20) ati ngosangalala chifukwa cha mphatso apatsidwa.
“Makamaka sopo andithandiza kuchapira matewera a khanda langali poti ndidalibe poyambira,” anatero Zuze.
Wolemba Cornelius Lupenga