Khalani osamala pamene mvula ya mphamvu ikugwa – DCCMS

Advertisement
Storm

Pamene Nthambi Yoona Zanyengo ya Department of Climate Change and Meteorological Services (DCCMS) yachenjeza aMalawi kuti mvula yamabingu ndinso yamphamvu igwa m’madera ambiri kuyambila Lachinayi mpaka Loweluka sabata ino, nthambiyi yachenjezanso anthu kuti akhale osamala makamaka m’madera omwe madzi amasefukila pafupi pafupi.

DCCMS yati mvula yamphamvu ndi yamabinguyi ili ndi kuthekera kobweretsa ziopsezo monga mphezi, mphepo yamkutho komanso madzi osefukira.

Nthambiyi yachenjezanso aMalawi kuti apewe kuwoloka mitsinje yomwe madzi ake akuthamanga kwambiri.

“Tiyembekezere nyengo ya mphepo ndi yamitambo komanso mvula ya mabingu yomwe ikuyembekezereka kugwa yamphamvu m’madera monga Mangochi ndi Ntcheu m’mawa uno,” yatero DCCMS.

Ndipo DCCMS yati masana a lero kukhala nyengo ya mphepo ndi yamitambo komanso mvula ya mabingu m’madera ambiri.

DCCMS yati anthu apewe kuusa mvula pansi pa mtengo ndipo mphepoyi ikuyembekezereka kuomba mwaphamvu pa nyanja za m’dziko muno.

Advertisement