M’tsogoleri wa chipani cha UTM a Dalitso Kabambe wati m’tsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera samadziwa kuyendetsa dziko ndipo chomwe amatha ndi kupemphetsa basi.
Polakhura ndi atolankhani kumasanaku, Kabambe anati zinthu zavuta m’dziko muno ndipo Chakwera alibe njira iliyonse yomwe atha kupanga kuti akonze zinthuzi.
Iwo anati zikuwoneka kuti boma la a Chakwera latha nzeru ndipo lilibe njira kapena mapulani othana ndi mavuto omwe a Malawi akukumana nawo kupatula kupemphetsa.
” Mafuta akasowa basitu kukapemphetsa, njala ikavuta basitu kukapemphetsa, forex ikasowa basitu kukapemphetsa. Kodi tizingokhalira kupempha? A Chakwera akuwoneka kuti alibe solution iliyonse ndipo zawakulira. Ngati m’tsogoleri amayenera kuyika njira zokhazikika zomwe zitha kuthana ndi mavuto omwe tikukumana nawo osati kumangoyenda mayiko akunja kukapemphetsa,” iwo atero.
A Kabambe alangiza Chakwera kuti asamangodalira kupemphetsa chifukwa kupempha sikungathetse mavuto omwe a Malawi akukumana nawo.
” Inu zowona m’tsogoleri wa dziko kumachita kunyadira kuti ndayenda mayiko 9 kupemphetsa ndi zonyadila zimenezi. Chakwera wapangitsa a Malawi kukhala opempha pempha, ndipo kupempha kulibe ubwino uliwonse mumangosawukilabe,” atero a Kabambe.
Malingana ndi Kabambe Chakwera akutichititsa manyazi a Malawi ndipo akuyenera kuvomeleza kuti walephera.