Mutharika wati chaka cha mawa abwezeretsa ma ofesi omwe anasamutsidwa ku Blantyre

Advertisement
Mutharika

Mtsogoleri wa kale wa dziko lino Peter Mutharika, wadzudzula chipani cha Malawi Congress (MCP) chomwe wati chikusambula nzinda wa Blantyre posamutsila ma ofesi ofunika ku Lilongwe. Iye wati chaka cha mawa akalowa m’boma, ma ofesiwa abweleraso ku Blantyre.

A Mutharika ayankhula izi ku mathero a sabata yatha pomwe chipani chawo cha Democratic Progressive (DPP) chinali ku hotela ya Golden Peacock munzinda wa Blantyre komwe chinapangitsa mwambo ofuna kupeza ndalama zothandizira ntchito zina za chipanichi.

A Mutharika ati ndizodandaulitsa kuti ulamuliro wa chipani cha MCP sukufunira zabwino nzinda wa Blantyre posamutsira ku Lilongwe ma ofesi ena a nthambi za boma.

“Ndimaukonda mzinda wa Blantyre chifukwa ndikomwe ndakulira. Ndimafuna mzindawu ukozedwe. Ndikudziwa kuti MCP pang’onopang’ono ikuwononga mzindawu posamutsa ma ofesi ofunika kupita ku Lilongwe.

“Ndikufuna ndikutsimikizileni kuti pa 17 September chaka cha mawa, ntchito yanga yoyamba ngati mtsogoleri wadziko lino, idzakhala kulamura kuti ma ofesi onse omwe asamutsidwa kupita munzinda wa Lilongwe, abwelere ku Blantyre,” watelo Mutharika.

Iye walonjezaso kuti akadzawina chisankho cha chaka cha mawa chino, adzamanga nyumba zingapo zosanjikizana munzinda wa Blantyre. 

Ena mwa ma ofesi omwe boma linasamutsira munzinda wa Lilongwe ndi monga; bungwe loyang’anila ntchito yofalitsa mauthenga la MACRA, bungwe loyendetsa chisankho la MEC, kungotchulapo ochepa chabe.

Advertisement