Tchamani wamapakulidwe osakhala bwino wachotsedwa ntchito ku Equatorial Guinea

Advertisement
Equatorial Guinea

Dziko la Equatorial Guinea lachotsa ntchito a Baltasar Ebang Engonga ngati mkulu wa National Financial Investigation Agency (ANIF) kutsatira kutchuka kwa makanema awo pa masamba a m’chezo.

A Ebanga atchuka pa masamba a m’chezo ndi makanema osakhala bwino, omwe amachita zachisembwere ndi azimayi osiyanasiyana mu office yawo komanso mahotela.

M’tsogoleri wa Dziko la Equatorial Guinea a Obiang Nguema Mbasogo ndi omwe analamula kuti tchamani yu achotsedwe ntchito chifukwa cha khalidwe lake losakhala bwino lomwe layipitsa mbiri ya dzikolo maka kwa anthu ogwira ntchito m’boma.

A Ebanga anazijambula akupakula katundu wa mkazi wachimwene awo, mchemwali wa m’tsogoleri wadzikolo, komanso azikazi a akulu akulu ena a m’dziko la Equatorial Guinea.

Makanemawo anapezeka pomwe achitetezo anakachita chipikisheni ku nyumba yake potsatira milandu ina ya katangale yomwe mkuluyu akuganizilidwa.

A Polisi wa anapeza makanemawa mu komputa ya mkuluyu. Makanemawa alipo ochuluka ndithu ndipo anthu akhala akatumizirana pa masamba a m’chezo.

Ankolowa akamachita madyedwewa azimayiwa amalola ndithu kuti azijambulidwa akupakulidwa. Azibambo komanso azimayi adabwa ndi khalidwe losakhala bwino la ankolowa.

Bamboyu ndi okwatila ndipo ali ndi ana asanu ndi m’modzi.

Advertisement