Makolo, ophunzira, agenda aphunzitsi kamba kakukomoka kwa ana atatu

Advertisement
Zomba

Chipwilikiti chinabuka pa sukulu ya pulayimale ya Chingale m’boma la Zomba pomwe ophunzira atatu adakomoka mosadziwika bwino Lachitatu m’mawa.

Izi zitangochitika, ophunzira komanso makolo ena okhudzidwa anayamba kugenda aphunzitsi ndi sukulu ati chifukwa chokwiya ndizomwe zikuchitikazi ndipo katundu wina waonongeka.

Apolisi anabwera kudzakhazikitsa bata ndipo pakadali pano maphunziro awayimitsa kaye ati pofuna kuti aphunzitsi pamodzi ndi makolo ayambe akambirana zatsogolo lankhaniyi.

Khansala wa m’dera la Chingale Michael Khwilipa watsimikiza zankhaniyi ndipo wati aka ndikachiwiri mwezi uno wa October kuti ophunzira amakalasi a sitandade 7 ndi 8 akomoke chifukwanso pa 9 mwezi omwe uno ophunzira enanso adakomoka.

Pakadali pano, ofesi ya zamaphunziro ya bomali sidayankhulepo kanthu pa zankhaniyi.

Advertisement