Patapita zaka pafupifupi zisanu malo okwelera galimoto pa tawuni ya Balaka asakugwira ntchito, adindo m’bomali tsopano alengeza za kuyambiranso kugwira ntchito kwa malowa.
Bwanamkubwa wa boma la Balaka, Tamanya Harawa watsimikiza kudzera mu chikalata kuti malowa tsopano ayamba kugwira ntchito lolemba likubwelari.
A Harawa ati chiganizochi chidapangidwa ndi ma khansala a m’bomali pa msonkhano wawo omwe unachitika posachedwapa.
Iwo apempha onse ochita malonda onyamula anthu pa magalimoto kuti ayambe kugwilitsa ntchito malowa akatsegulidwa ndipo yense onyozera adzalipilitsidwa chindapusa cha ndalama yokwana K50,000.
Koma m’modzi wa oyendetsa galimoto zonyamula anthu m’bomali Sandram Phiri watiuza kuti sakugwilizana ndi lingaliro la khonsoloyi ndipo ati adakakonda adindowa adakawalora kuti azipitilira kupakira anthu panja pa malowa.