Gotani-Hara atenga mpando wa Wachiwiri oyamba wa mtsogoleri wa chipani cha MCP

Advertisement
MCP

A Catherine Gotani Hara omwenso ndi sipikala wa nyumba ya Malamulo, atenga udindo wa Wachiwiri oyamba wa mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress ku msokhano wa ukulu wa chipanichi ku Bingu International Convention Centre (BICC) – Lilongwe.

Kunali nkokenkoke kumasanaku pamene ena anali ndi nkhope zozyolika komanso ena kukondwa kamba koti apeza udindo mchipani cha MCP.

Pamene lero kumacha nkuti ma deligetsi ambiri atatoperatu kamba koti dzulo usiku mwayi agona unali obera. Koma chomwe chidali chochititsa chidwi nchakuti mtsogoleri wa dziko lino yemwenso ndi mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress, a Lazarus Chakwera sadawodzere usiku wonse kuonetsetsa kuti zisankho ziyenda bwanji.

Mmawa wa lero ntchito imene idakula idali kuwerengera ma voti ndipo ma kandideti mitima inali mmwamba. Zotsatira zosatsimikizika zitayamba kumveka, otsatira amakandideti ena amangotuluka mu BICC mwakachetechete akazindikila kuti kandideti wawo zamuvuta.

Ndipo ku mbali ina anthu ngati a Richard Chimwendo Banda omwe amaimila udindo wa Mlembi wamkulu wa chipani cha Malawi Congress, amapatsidwa moni ena kululutira, pozindikila kuti a Richard Chimwendo Banda zawayendera pa udindowu.

Nawo a Catherine Gotani Hara, omwe amaimila pa udindo wa Wachichiwiri kwa mtsogoleri wa chipanichi, adayamba kupatsidwa chanza kamba koti zawo zidali zitayeranso.

Zotsatira zimene a Malawi Electoral Commission (MEC) aperekera pa zisankhozi ndi zoti; udindo wa Wachiwiri oyamba wa mtsogoleri wa chipani cha MCP wapita kwa mayi Catherine Gotani Hara. Udindo wa Mlembi wamkulu wa chipanichi wapiti kwa a Richard Chimwendo Banda ndipo a John Paul atenga udindo wa Msungichuma. A Jessie Kabwira atenga udindo wa Ofalitsa nkhani mchipanichi.

Udindo wa Mkulu wa Amayi wapiti kwa a Jean Sendeza ndipo udindo wa Mkulu wa achinyamata atenga ndi a Steven Baba Malondera. Udindo wa Mkulu owona nkhani zokhudza malamulo a Jivason George Kadzipatike atenga udindowu.

Udindo wa Mkulu owona za chuma atenga ndi a Henry Mumba ndipo a Elias Chakwera atenga udindo wa Mkulu oyendetsa zisankho. Udindo owona za maubale ndi anthu wapita kwa a Sam Dalitso Kawale.

Advertisement