Anthu okwiya ku dera la Katlehong, Johannesburg m’dziko la South Africa awotcha tchalitchi cha mneneri Paseka Mboro Motsoeneng.
Malingana ndi nyumba zofalitsa nkhani m’dziko la South Africa, anthu okwiyawa achita izi pokwiya kuti Mboro anapita pa sukulu ya Matsediso Primary mderalo kukalanda ana ake awiri amene amakhala ndi agogo awo omweso ndi mphunzitsi pa sukuluyi.
Anthu kuphatikiza ana pa sukulupo anakwiya kamba koti mneneriyu anafika pa sukulupa mwamavuvu kwinaku atanyamula zikwanje pamene wachitetezo wake ananyamula mfuti ya mtundu wa AK47.
Khwimbi la anthuwa linatutana ndikuthamngira ku nyumba kwa Mboro yemwe anali atathawira kale ku polisi kukabisara. Posagonja, anthuwa lero Lachiwiri anapita ku tchalitchi cha mneneriyu chomwe achiwotcha.
Potsatira izi, apolisi amanga Mboro komaso anthu ena angapo pokhudzidwa ndi ziwawa zomwe iwowa anachita potenga zikwanje nkukaopseza ana pasukuluyo.