Mulibe mphamvu yoletsa anthu kukapikisana nawo – Khothi lawuza MCP

Advertisement
MCP

Pomwe mamembala ena analetsedwa kudzapikisana nawo pa mipando yosiyanasiyana pa mkumano waukulu wa chipani cha Malawi Congress, oweruza ku bwalo lalikulu a Howard Pemba wagamula kuti komiti yaikulu ya chipanichi ilibe mphamvu zoletsa ma membala ena achipanichi kuimila pa maudindowa.

Izi zikutsatira chiganizo chomwe anthu omwe analetsedwawa anachita pokamang’ala ku bwalo lalikulu kuti liwunikire za nkhaniyi patangodutsa maola ochepa chabe pomwe komiti yaikulu ya chipanichi inalengeza maina a wanthu omwe ali ololedwa kukapikisana nawo pa ma udindo osiyanasiyana.

M’modzi mwa ma membala achipanichi omwe adachotsedwa pa ndandandawu ndi a Vitumbiko Mumba. A Mumba akhala akupanga kampeni osadziwa kuti achotsedwa pa mndandanda wa anthu okaima nawo ku convention.

Polankhula lero pa msokhano wa atolankhani, komiti ya chipanichi inati iyo siiyang’ana umembala wa chipani okha, koma imayang’ananso ngodya zachipani monga kukhulupilika. Komitiyi idati ilibe nazo ntchito zomwe zitabwere kuchokera ku khothi.

Pamene komiti imachititsa msokhano wa atolankhani ku Lilongwe, nkuti nkhani ili nkati ku khothi. A Judge Pemba anati komitiyi yasintha malamulo a chipani cha Malawi Congress zomwe sizoyenera.

Kudzera paganizo la komitiyi loti anthu atsopano mchipani komanso omwe sadakhalepo ndi udindo uliwonse asapikisane nawo, a Pemba anati ili siganizo loyenera.

Bwalori lati chiganizo cha komitiyi chikuphwanya ufulu wa mamembala omwe sadapatsidwe mpata okhala ndi anthu omwe akuwafuna, pa mndandanda wa opikisana.

A Pemba anati m’malamulo akulu oyendetsera chipani cha MCP mulibe malamulo okhudza zomwe komiti yaikulu inalengeza zoletsa kuti ena asapikisane nawo pa chisankho ku convention.

Anthu ochuluka akhala akutsutsa ganizo la komiti ya chipanichi kamba kakuti yemwe ali mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera adaima pa mpando wa mtsogoleri wa chipanichi m’mbuyomu, ndipo panthawiyi anali asanakhalepo membala wa chipani chi.

Ndipo madzulo ano, a Mumba achititsa msokhano wa atolankhani kuti ayankhulepo pakusiyidwa kwawo pa mndandanda okaimila ku mkumano waukuluwu.

Advertisement