Ku MCP kwatelera! Alex Major wati pavute pasavute akukayima kukonveshoni

Advertisement
MCP

Alex Major yemwe ali mgulu losiyidwa pa mndandanda wa anthu omwe akuyenera kupikisana nawo ku msonkhano waukulu wa chipani cha Malawi Congress (MCP), wanenetsa kuti zivute zitani akapikisana nawo, ndipo wati iye nde oyenera pa udindo wa ulembi wa chipanichi.

Major wati sakutekeseka ndizomwe zachitika lero pomwe akuluakulu a chipanichi awachotsa iwo ndi anthu ena pa mndandanda wa anthu omwe akukapikisana ku konveshoni yomwe iyambe Lachinayi sabata ino mpaka Loweluka.

Iwo ati, “Ndichikhulupiliro changa kuti ine pa 8 pano ndikhala pa ballot ndipo ndiimilira nawo zisankho zimenezi. Tonse tili muno ndi aMalawi chotsatira chomwe chimakhalapo ngati munthu satsatira chigamulo cha bwalo la milandu ndi chiyani?

“Ine sindikuwaopa onsewo, ine ndi wabwino kuposa onsewo. Mwa chitsanzo, enanu mwawadziwa a Simplex Chithyola zaka ziwiri zapitazi. Ineyo dzina langa silisowa, palibe oti alisowetse.”

Komiti yayikulu ya chipani cha MCP imafuna kuletse anthu omwe sadakwanitse zaka ziwiri ali mchipanichi kuyimira nawo pamaudindo akuluakulu zomwe bwalo la milandu lagamula kuti zisachitike ponena kuti ndikuphwanya malamulo a chipanichi.

Lachiwiri oweruza milandu Howard Pemba wagamula kuti mamembala a chipanichi ndi omwe ali ndi mphavu komanso kuthekera kosankha munthu yemwe akufuna osati potengera chiganizo cha komiti ya ukulu.

Advertisement