Aphunzitsi okwana 59 m’boma la Thyolo adandaula kuti sanalandilebe ndalama zawo za alawasi patadutsa pafupifupi miyezi iwiri chigwilireni ntchito yoyang’anira mayeso a Junior Certificate of Education (JCE).
Aphunzitsiwa ati ndalamazi amayenera kulandira mayesowa asanayambe koma mpaka pano kuli zii ndipo posachedwapa mphunzitsi wina mwa iwo anamangidwa kamba kokumbutsa ndalamazi.
M’modzi mwa aphunzitsi odandaulawa watiuza kuti mpaka pano bungwe la Malawi National Examination Board (MANEB) silinawapatsebe ndalamazi ngakhale kuti aphunzitsi anzawo omwe anayang’anira mayeso a MSCE omwe atha pa 26 July 2024 anapatsidwa ndalama zawo mayesowa asanayambe.
Mphunzitsiyu wati, “Panopa tonse tafika potopa ndikukumbutsa. Zafika poti akuluakulu ena tikakumbutsa akumatiopseza mpaka m’modzi waife anamangidwa pa 5 July ndikutulutsidwa pa 8 July 2024 chifukwa chokumbutsa ndalamazi kudzera pa gulupu ya WhatsApp yomwe inapangidwa.
“Munthuyu analemba pa gulupupo kuti ‘ndalama zangazo mudye ndisakhale ngati ndikupempha pamene ndinagwira ntchito. Ngati munadya kale matembelero anu amenewo,’ atatelo anatuluka pa gulupupo.
Ofesala wina analemba kuti ‘zalowa personal, ndithana nawe,’ ndipo kenaka mzathuyu anamangidwa pa mlandu wonyozana pa intaneti (cyberbullying).”
Pomwe tinafuna kumva ngati akudziwa za kwa mphunzitsiyu, Rebecca Misiri yemwe ndi Chief Education Officer wa boma la Thyolo wati tifuse zankhaniyi mneneri wa khonsolo ya bomali, ndipo kuonjezera apo, pa nkhani yakuchedwa kulipira aphunzitsiwa ma alawasi awo, anatiuza kuti tiyankhule ndi akuluakulu a bungwe la MANEB.
Ofalitsa nkhani ku bungwe la MANEB Angella Kashitigu, anatibwezaso kuti tiyankhule ndi mkulu wa maphunziro m’bomali a Rabson Kawalala omwe anati sangayankhule zambiri kamba koti atenga udindowu posachedwapa kuchokera m’boma la Mangochi.
Komabe a Kawalala anati akuganiza kuti mwina aphunzitsiwa achedwa kulandira ndalama za ma alawasizi kamba koti Thyolo ndi limodzi mwa maboma omwe aphunzitsi akumalipilidwa kudzera m’njira za makono ndiye mwina nkutheka ena analakwitsa ma nambala awo aku banki.