Chilima anatisiya ali m’boma ineso ndikhala momwemo – wanenetsa Usi

Advertisement
Government through the Minister of Natural Resources and Climate Change Michael Usi has underscored the need for more awareness on climate change issues especially for people in rural areas.

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino,  Michael Usi, yemweso ndi mtsogoleri ogwilizira wa chipani cha United Transformation Movement (UTM) wati sasiya kugwira ntchito ndi a Lazarus Chakwera ponena kuti iwo akuchita zomwe malemu Saulos Chilima anakachita.

Usi wayankhura izi Lolemba ku kunyumba ya boma ya Mudi mu nzinda wa Blantyre komwe potsazikana ndi otsatira chipanichi wanenetsa kuti iwo sasiya kugwira ntchito ndi a Chakwera ngati momwe akuluakulu ena achipani cha UTM akufunira.

“Chikundidabwatsa nchoti akuti ndikugwira ndi a Chakwera siwa UTM, kodi ananditengera kukagwira ntchito ndi a Chakwera ndi ine? Anali bwana athu a Chilima. M’mene a Chilima amatisiya anali ali m’boma tsopano iwowo apita nde ine ndizikati ndachokamo? Nanga ndikakakumana nawo nde akakandifusa kuti ndinachoka chifukwa chiyani ndi zikati chiyani?” watelo Usi.

Iwo adzudzulaso akuluakulu ena a chipani cha UTM omwe akuti akumawatokosora dala ndicholInga choti pakhale mikangano, zomwe anenetsa kuti sangapange.

Usi wati, “Tikayamba kukangana kenaka nkudzakondana anthu otiona adziti opusa awowo. Ndiye ine sindikufuna zokangana ndi aliyese, sindikangana nawo kaya anena nyenwa kaya sanena koma ineyo ndikufuna kuti zimene amafuna Dr Chilima m’dziko muno zichitike.”

Mtsogoleri wa UTM-yu walangiza akuluakulu a chipanichi kuti ngati pali pena pomwe sakumvetsa ndi bwino awafikire ndikuwafuse iwo kuti mchipanichi mupitilire kukhala bata ndi mtendere. 

Zonsezi zikubwera kutsatira msonkhano wa ndale wa chipanichi ku Mzuzu Lamulungu lapitali komwe mlembi wa UTM Patricia Kaliati anati mamembala eni eni a chipanichi ndiokhawo omwe akumapezeka pa misonkhano yawo osati omwe akukakamila kukhala m’boma. 

Advertisement