Mboni yati Bushiri sadalandire ndalama zobedwa

Advertisement
Prophet Shepherd Bushiri and Wife Mary Bushiri Walking

Sibongire Mnzinyathi yemwe ndi mkulu ozenga milandu ku Gauteng Province m’dziko la South Africa wauza bwalo la milandu kuti palibe kampani ya Mneneri Shepherd Bushiri ndi nkazi wake Mary yomwe inalandira ndalama zobedwa.

Izi zadziwika pomwe lero Lolemba ma loya a Bushiri kuphatikizapo Annellen Van Den Heever, anapitilira kufunsa mafuso a Mnzinyathi molingana ndi umboni omwe unaperekedwa kubwalo la milandu okhudza mlandu ozembetsa ndalama omwe a Bushiri akuganizilidwa kuti anapalamura ali m’dziko la South Africa.

Poyankha mafunsowo, mkulu wozenga milandu ku Gauteng Province-yu anavomeleza m’bwaloli kuti tchalitchi komanso ma kampani a Mneneri Bushiri ndi nkazi wake sanalandire ndalama zilizonse zomwe zinali zobedwa.

Izi zikutsutsana ndi lipoti la kafukufuku yemwe inachita ndi kampani ya KPMG lomwe linafotokoza kuti kampani za oganizilidwawa zinkalandira ndalama kuchokera ku kampani ya Rising Estate yomwe ikuganizilidwa kuti inkabera ndalama anthu opemphera.

Lachisanu lapitali Van Den Heever anauza atolankhani munzinda wa Lilongwe kuti akukhulupilira kuti wakwanitsa kubweretsa poyera momwe a Mnzinyathi akhala akupelekera maumboni onama ku bwalo la milanduli.

Pakadali pano mlanduwu wayimitsidwa kaye kufikira Lachitatu sabata ino pomwe oyimilira boma pa mlanduwu, Dzikondiathu Malunda akakhale akukoza zina zomwe a Mnzinyathi akhala akuyankhula kudzera mukuwafunsa mafunso.

Advertisement