Chipani chotsutsa boma cha Democratic Progressive (DPP) chatsimikiza za kutuluka m’chipani kwa a Dalitso Kabambe, koma chati sichikudandaula ponena kuti ngakhale banja limene limatha ndipo aliyese amalowera kwake.
Potsatira kalata yomwe a Kabambe omwe anakhalaposo gavanala wa banki ya ikulu ya Reserve atulutsa Lolemba yolengeza za kutuluka m’chipanichi, DPP yalemba pa tsamba lake la fesibuku kutsimikiza kuti kalatayi yafikadi ku chipanichi.
Ngakhale zili choncho, chipanichi chati sichinganene zambiri pa nkhaniyi ponena kuti aliyense ali ndi ufulu okhala mchipani chomwe akufuna ndipo chiganizo chomwe achita a Kabambe achilandira.
Chipani cha DPP chati: “Tadziwitsidwa za kutuluka mchipani kwa a Dalitso Kabambe ndipo chipani chathu chikufuna kuyankhapo. Timakhulupirira kwambiri ufulu wosonkhana ndipo timalemekeza ufulu wa munthu aliyense wosankha yekha zochita. Chifukwa chake, tilibe chinthu chenicheni choti tingayankhule pa nkhaniyi.
“Chipani chathu chikudziperekabe ku mfundo za demokalase ndipo chidzapitiriza kusunga mfundo za ufulu ndi kufanana kwa anthu onse.”
Kupatula kulemba pa fesibuku, mneneri wa chipanichi a Shadric Namalomba awuza nyumba zina zosindikiza nkhani m’dziko muno kuti palibe chodandaulitsa ponena kuti ngakhale banja limene limatha, mwamuna kapena mkazi amatha kukakwatira kwina.
A Namalomba atsutsaso mphekesera zomwe zikuveka kuti kutuluka m’chipani kwa a Kabambe ndi kamba koti mtsogoleri wa chipanichi, a Peter Mutharika akukapikisana nawoso ku konveshoni ya chipanichi mwezi wa mawa uno.
Pakadali pano a Kabambe sanalengeze za tsogolo lawo pa ndale koma mphekesera zikuveka kuti akulowera ku chipani cha United Transformation Movement (UTM) komwe zikuveka kuti akukalowa m’malo mwa mtsogoleri wa chipanichi malemu Saulos Chilima omwe anafa mwezi watha pamodzi ndi anthu ena 8 pa ngozi ya ndege.