Banja lina lanjatidwa kamba koba khanda

Advertisement
Kamuzu Central Hospital

Apolisi ku Lilongwe amanga banja lina lomwe akuliganizira kuti linaba khanda la masiku awiri pa chipatala chachikulu cha Kamuzu.

Malinga ndi Mneneri wa polisi ku Lilongwe a Hastings Chigalu, a Wyson komanso Gloria Misoya, onse a zaka 32, akhala pa banja kuchoka mchaka cha 2022 opanda mwana chifukwa mayiyo adatenga njira ya kulera yoti asazabelekenso.

A Chigalu anapitiliza kunena kuti bambowo akhala akukakamiza mayiyo kuti abeleke.

“Chifukwa chokakamizidwa a mayiwo anakonza mimba yabodza ndipo pa 12 October, bamboyo adatengera mayiyo ku chipatala cha Bwaila kokachira ngakhale bamboyo amadziwa kuti mayiyo alibe mimba,” atero a Chigalu.

Malingana ndi a Chigalu, banjali litafika Ku Kamuzu Central, mayiyo anapita ku khitchini komwe anapeza Gogo wina atanyamula khanda la mdzukulu wake ndipo apa mayiyu anapempha Gogoyo kuti amulandire khandalo lomwe atapatsidwa mayiyo sanachedwe koma kuwuza Gogoyo kuti akukagula Mango koma cholinga chake chinali chofuna kuba mwanayo ndipo atapatsidwa nkhandalo sanabwelereso ulendo unali omwewo.

Anthu a mmudzi ndiomwe anakaneneza banjalo ku polisi atawakaikira. 

Pakadali pano a Polisi abweza khandalo kwa makolo ake. 

Ngakhale amafunitsitsa mwana wina bambowa ali kale ndi ana awiri kuchoka ku banja lawo lina lakale ndipo mayiyu alinso ndi ana awiri kuchoka ku banja lina.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.