Nepman adzudzula oimba anzake za nsanje

Advertisement
Nepman to release Amapiano song

Oyimba Nepman yemwe dzina lake lenileni ndi Neppier Longwe wadzudzula oyimba anzake omwe akumaonetsera mkhalidwe wa nsanje mmayimbidwe a m’dziko muno.

Nepman, yemwe padakali pano ali m’dziko la Zambia wayankhula chomwechi kudzera pa tsamba lake la mchezo la Facebook pomwe wati anthu amene akumuchitira nsanje wa anamupeza ndipo azamusiwa mmayimbidwe.

Chomwe chatsitsa dzaye kuti njobvu itchoke nyanga nchakuti atakumana ndi oyimba wina m’dzikolo anamuuza kuti wakhala akusaka nambala yake ya lamya kwa oyimba ena ochokera kuno omwe amapitapita ku Zambia koma amayankhidwa kuti alibe pomwe ali nayo.

“Mu industry ya music ku Malawi inachuluka nsanje maka kwa oyimba tokhatokhafe ma artist ena anzanga ochokera ku Malawi atabwera kuno ku Zambia akhala akupemphedwa nambala yanga koma zachisoni anthuwo amayankha kuti nambala yanga alibe pomwe alinayo,”watero Nepman 

Ndipo Anapitilira kufotokoza kuti” Nde anthu omwewo akudabwa mmene ndikupelekera ma nambala a oyimba anzanga.Ndinkona oyimba ena akuluakulu amakhomelera ma upcoming artist kuopa kuti awaposa.”

Katswiri wa nyimbo ya “Nalero” wafika dzulo ku Zambia, kupyolera pa tsamba lake la Facebook taona atajambulitsa ndi B1 yemwe ndi oyimba odziwika bwino m’dzikolo.

Palinso mphekesera zonena kuti Nepman, Queen Sheba komanso B1 akupanga nyimbo imodzi.

Advertisement