Bungwe lowona za ufulu wa anthu la Malawi Human Rights Commission (MHRC) lati makolo a mwana wa sabata zisanu ndi ziwiri yemwe anamwalira pa chipikisheni cha Mtambalika (road block) m’boma la Mzimba mwezi wa June 2023 asumire wapolisi omwe analetsa galimoto kudutsa kuti aperekeze mwanayo kuchipatala.
Malingana ndi lipotili, Mwanayo anamwalira potsatira kuchedwetsedwa kufika naye kuchipatala komwe kunachitika ndi apolisi apansewu pa malo ochitira chipikisheni, omwe akuti adapempha ndalama kwa dalaivala wa taxi ngati chindapusa.
M’modzi mwa makomishonala a bungwe la MHRC a Boniface Massah, anena izi ku Lilongwe pomwe bungweli limapereka lipoti lake pa kafukufukuyu pa zomwe zidapangitsa kuti mwanayo amwalire.
Komishonala Massah adati banja la mwana yemwe anamwalirayu liri ndi ufulu wotengera wapolisi yemwe adakaniza galimotoyo kudutsa ku khothi.
Massah adatinso bungwe la Police Independent Complaints Commission lifufuze apolisi omwe anali pa chipikisheni cha Mtambalika pa tsikulo.
Bungwe la MHRC mulipoti lakelo laonjezera kuti apolisi a mogwirizana ndi nthambi ya Road Traffic and Safety Services alimbikitse kuphunzitsa anthu za malamulo apamsewu, makamaka makamaka oyendetsa ma taxi.
Bungweli lati likuyembekezeka kuti mfundo zomwe lapereka zitsatidwe mkati mwa miyezi itatu kuyambira pa 9,Julayi,2024.
Poyankhulapo pa zalipotili, wapampando wa mabungwe womwe asali aboma ku Mzimba , Christopher Melele wati ndiwokondwa ndi lipotilo.
“Ife ngati amabungwe womwe si aboma kuno ku Mzimba ndife wokondwa kwambiri ndilipotili la MHRC, lipotili lachita kuneneratu kuti apolisi adalakwitsa, tiyamikire bungwe la MHRC ponena chilungamo, zomwe zili mulipotili ndizomwe anthu amayembekezera,” Anatero a Melele.
Malawi24 yapeza kuti wapolisi yemwe adakaniza galimoto yomwe inanyamula mwana wodwalayo ndi Sub.Inspector Masatso Zigwetsa yemwe amagwira ntchito ku nthambi ya polisi ya pamseu (Road Traffic), pakadali wapolisiyu anasamutsidwa ku mzimba.
Anthu, kuphatikizapo mabungwe ambiri anadzuzula kwambiri wapolisi yemwe analetsa galimoto yomwe ina nyamula mwana kupita naye kuchipatala chachikulu cha Mzimba kuti umunthu alibe, panthawiyo nkuti mwanayo amataya magazi.