A Biden achita chibwibwi, Trump awala pa m’tsutso oyamba wa otsogolera America

Advertisement
Joe Biden

Pulezidenti wa dziko la America Joe Biden anachita chibwibwi kangapo konse pa m’tsutso woyamba wa Pulezidenti usiku wa pa 27 June, 2024.

 A Biden anakanika kuyankha mafunso nthawi zina ndipo analephera kufotokoza malingaliro awo moveka bwino. Mtsutso womwe udakumanitsa iwo ndi pulezidenti wakale wadzikolo yemwenso ali woyimilira chipani cha Republican Donald Trump, amachitkira ku Atlanta, Georgia. 

Mwazina zomwe zinamanga nthenje pa mtsutsowu ndi kukwera kwa zinthu, nkhani zokhuza nthambi yakuwona kolowa anthu mdzikolo, chitetezo cha chamalire adzikolo, nkhani zakuchotsa mimba pakati azimayi ndi zina za mbiri. 

donald-trump
Donald John Trump

Potsatira mtsutsowu, nyumba zina zowulutsa mau zati a Biden amakanika kuyankha mafunso bwino kamba kakuti anali akudwala chimfine.

Pulezidenti Biden, omwe ali ndidzaka 81, adavutika kwanbiri kuti ayankhe mafunso pomwe a Trump, ochepera zaka zitatu kuposa a Biden, adawoneka omasuka poyankha mafunso mwaukadaulo pamtsutso wa mphindi 90 womwe unakonzedwa ndi kanema ya CNN.

A Trump adatchula a Biden ngati Pulezidenti woyamba m’mbiri ya dziko la America yemwe walepheleratu kuyendetsa dziko, iwo anapereka chitsanzo cha kukwera kwa zinthu kuphatikizapo nkhondo zaku Ukraine ndi Gaza.

A Biden womwe anthu amayembekezera kuti achita bwino pa msutsowo anabvutika kupereka mfundo zamphamvu, ndipo anapereka mpata kwa Trump kuti awale.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.