
Pakuwoneka panali kusamvana pakati pa apolisi maka pa komwe wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive (DPP), mchigawo cha pakati, a Alfred Gangata akazengedwere pomwe mlandu wawo awusamutsila ku bwalo la Nkukula ku Lumbadzi m’boma la Dowa.
Poyamba a Gangata anafika nawo ku bwalo la milandu la Lilongwe ku area 3 komwe mosakhalitsa ananyamuka nawo mu galimoto la Ambulance kupita nawo ku Dowa.
Oyimilira a Gangata pa milandu a Gilbert Khonyongwa awuza nyumba zina zowulutsa mawu kuti pakuwoneka pali kusamvana pa apolisi omwe akuyendetsa mlandu wa a Gangata.
Wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha DPP yu anakadzipeleka yekha ku polisi Lolemba atamva zoti apolisi akumufuna pa mlandu omuganizila kuti amagwiritsa ntchito satifiketi ya MSCE yomwe anaipeza mwachinyengo pa sukulu ya Chitowo, ndipo adamutsekera mchitolokosi.
Posachedwapa a Gangata anawamanganso ati pa mlandu osema zikalata zabodza za ku bungwe lotolera msonkho la Malawi Revenue Authority (MRA) kuti apambanile ntchito ku sukulu ya ukachenjede ya LUANAR mzaka za 2017/2018.