Misonzi yathu ifufuzidwa mosabisa komanso mwapadera – Chakwera

Advertisement
Mary Chilima

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ati akumvesetsa kuti aMalawi akulira ndipo misonzi yawo siipita pachabe kamba koti boma lifufuza bwino infa ya wachiwiri wa mtsogoleri wa dziko lino Dr Saulos Chilima.

A Chakwera amayankhura izi pa bwalo la za masewero la Bingu pamene mwambo wopeleka ulemu kwa wachiwiri wa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima wachitikira.

Iye wati wapempha kale akatswiri a maiko a kunja kuti athandize dziko lino kupanga kafukufuku kuti ndege yomwe anakwera a Chilima komanso ena asanu ndi atatu ichite ngozi.

Lazarus Chakwera
Kafukufuku wapadera achitika – Chakwera.

“Ndikukutsimikizirani kuti kafukufuku wapaderayu achitika ndithu. Ndipo tiyesetsa kuti tidziwe chenicheni chomwe chinachitika chifukwa inenso ndikufuna ndidziwe poti ndili ndi mafunso ochuluka ofuna mayankho,” anatero aChakwera.  

Iwo ati nthawi yamavutoyi kukhala mayankhulidwe osakhala bwino, kunyozedwa, kutonzedwa komano munthu aliyense ayenera osazitengera chifukwa uko ndikulira kwa anthu omwe asweka mtima. 

A Chakwera ati ngati kholo, akuyenera kuvomereza zonsezi chifukwa munthu olira saletsedwa kutero.

 “Ifeyo tiyenera tikhale otonthozana osati kubwenzera ayi. Tataya munthu osasunga mangawa, opilira komanso ofunikira kwambiri ndipo imfa imeneyi tiyimva kuwawa kwa nthawi yaitali,” anamaliza motero.

Nduna yaikulu ya kale ya dziko lino la Kenya a Raila Odinga ati malemu Chilima anali a chinyamata kwambiri ndipo Kenya ikulira limodzi ndi Malawi pamene yataya mtsogoleriyu.

A Odinga ati malemu Chilima wachita zinthu zambiri pamoyo wake kuno ku Malawi komanso maiko omwe iye amapita pofunitsitsa kuti Africa akhale ogwirizana ndipo adzawakumbukira malemuwa ngati munthu modzi olimbikira pa ntchito yake. 

A Chilima komanso a Shanil Dzimbiri ndi Chisomo Chimaneni (Ntchisi), Dan Kanyemba (Lilongwe), Colonel Owen Sambalopa (Zomba), Major Wales Aidin (Mangochi), Flora Selemani Ngwirinji (Thyolo) and Lukas Kapheni (Kasungu), anamwalira pa ngozi ya ndege yomwe inachitika lolemba mu nkhalango ya Chikangawa m’boma la Mzimba.

Ena mwa anthu omwe abwera pa mwambowu ndi mtsogoleri wakale a Joyce Banda, wachiwiri wa mtsogoleri wakale ,Khumbo Kachale, Shepherd Bushiri, komanso atsogoleri ochokera ku Kenya, Zimbabwe, Congo komanso kuzipani yosiyanasiyana monga Alliance for Democracy (AFORD),United Transformation Movement(UTM) ndi ena.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.