Bungwe lowunika mauthenga la Malawi Communications Regulatory Authority (MACRA) ladzudzura mchitidwe otumizirana zithunzi zowopsa za ngozi ya ndege yomwe yachitika Lolemba m’dziko.
Malingana ndi kalata yomwe wasayinira ndi mkulu wa bungwe la MACRA a Daud Suleman, m’masamba amchezo ochuluka anthu akugawana zithuzi zangozi ya ndege yomwe yapha anthu 9 kuphatikizapo wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko la Malawi Dr Saulos Klaus Chilima.
Bungweli lakumbutsa anthu m’dziko muno kuti kutumizirana zithunzi zosakhala bwino ndi mlandu ndipo lalangiza anthu kuti apewe mchitidwewu pa nthawi ino yachisoni ponena kuti zithunzi zotele zimawonjezera kusweka mtima pakati pa anamalira.
“Komabe, tili okhudzidwa kwambiri ndi kufalitsidwa kwa zinthu zosakhala bwino komanso zopeleka mantha zokhudzana ndi ngoziyi. MACRA pansi pa Gawo 97 la Electronic Transactions and Cybersecurity Act inapatsidwa mphamvu kuti ilimbikitse maphunziro a anthu pazakhalidwe labwino pa intaneti. Tikulimbikitsa anthu kuti azisamala kwambiri ndikupewa kugawana kapena kufalitsa zinthu zowopsa,” yatelo mbali ina ya kalatayi.
A Chilima pamodzi ndi anthu ena asanu ndi atatu afa Lolemba pa 10 June 2024 pomwe ndege yomwe anakwera popita ku maliro a loya Ralph Kasambara inagwa ku mbali ina ya nkhalango ya Chikangawa m’boma la Mzimba.