Anthu ogwira ntchito za umoyo mzipatala zosiyanasiyana mdziko lino ayimitsa ntchito zawo lero ndipo ali mkati mwa zionetsero zofuna kukamiza boma la Malawi kuti liwakwezere malipiro awo.
Izi zikudza kutsatira chikalata chomwe wasayinira ndi wapampando wa bungwe la National Organisation of Nurses and Midwives (NONM), Shouts M. Galang’anda Simeza komanso wapampando ku bungwe la Physician Assistance Union of Malawi (PAUM), Solomon David Chomba ponena kuti sabweza ganizo lawo lochita kunyanyala ntchito lero.
Malingana ndi kalatayi, iwo ati apitlira ndi ganizoli pamene boma silikufuna kumva madandaulo awo.
Iwo ati akufuna boma liwakwezere malipiro pomwe zinthu zakwera mtengo zomwe zikupangitsa moyo wawo kukhala ovuta.
Pakadali pano kunyanyala ntchitoku kuli mkati pa chipatala cha Salima ndipo Malawi24 inayankhula ndi m’modzi mwa ogwira ntchito pachipatalachi yemwe anati tisamutchule dzina, anati ogwira ntchitowa anapereka madandaulo kuboma ndipo mpaka pano sadayankhidwebe.
“Nkhaniyi yakhala ikukambidwa kuti tikufuna boma litikwezere malipiro athu koma mpakana lero boma silinamvebe madandaulo athu apa mchifukwa chake mukuona anamwino akuchita zionetsero.”
Malawi24 inayankhulananso ndi m’modzi amene wabwera kudzalandira thandizo pachipatalachi ndipo wati akupempha boma kuti liganizire kukonza vutoli mwachangu.
“Boma litiganizire pa zomwe zikuchitikazi chifukwa titha kuluza mimoyo ya anthu ambiri chifukwa cha zionetsero zomwe zikuchitikazi,” anatero Wilson Yona yemwe anabwera kudzalandira thandizo pachipatalachi.
Mabungwe a PAUM komanso NONM adanena izi mwezi watha wa May kuti ogwira ntchito mzipatalawa ayamba kunyanyala ntchito lero.