Lucius Banda apha mphekesera za imfa yake ndi uthenga wachilimbikitso

Advertisement
Lucius Banda

Pomwe anthu ena amafalitsa mphekesera kuti woyimba Lucius Banda wamwalira, mkhalakale pa mayimbidweyu wayankhula kwa omutsatira pa tsamba lake la fesibuku. 

Banda yemwe amadziwika ndi dzina loti Soja ali m’dziko la South Africa komwe akulandira thandizo la mankhwala pa nthenda ya ipso yomwe wadwala kwa ka nthawi tsapano.

Koma pomwe mphekesera yoti woyimbayu wamwalira inakula kumathero asabatayi, Lolemba Soja walimbikitsa omutsatira pa tsamba lake la fesibuku kuti adzikhulupilira Mulungu yekha basi.

Mu uthenga wake omwe walemba mchingerezi, Banda wagwilitsa ntchito buku la m’Baibulo la Yeremiya  pa mutu 17, ndime ya 7 mpaka 8.

“Wodala munthu amene akhulupirira Yehova, amene chikhulupiriro chake ndi Yehova. Ndipo adzakhala ngati mtengo wooka kuli madzi, wotambalitsa mizu yake pamtsinje, wosaopa pofika nyengo yadzuwa, koma tsamba lake likhala laliwiri; ndipo suvutika chaka cha chilala, suleka kubala zipatso.” 

Chifukwa cha kudwala, Banda wakhala nthawi asanabwele poyera zomwe zinapangitsa anthu ena kufalitsa nkhani yoti woyimbayu wadzala chinangwa.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.