Bwalo lamilandu munzinda wa Lilongwe, lapeza mayi Anne Debre Mumba olakwa pa mlandu omwe amayankha wakupha amunawo malemu pulofesa Peter Mumba.
Malemu pulofesa Mumba omwe anali mphunzitsi pa sukulu yaukachenjede ya Bunda, anamwalira mchaka cha 2020 atadwala kwa nthawi yochepa kwambiri.
Potsatira kupimidwa kwa thupi lawo ndi achipatala, nkazi wa malemuwa Anne anamangidwa poganizilidwa kuti ndiye anapha pulofesa Mumba powapatsa chakudya chomwe amaganizira kuti munali poyizoni.
Bwalo la milandu lakhala likumva mbali zonse zokhudzidwa kufikira Lachinayi sabata ino pomwe lapeza mkazi wa malemuyu wolakwa pa mlandu wakupha amunake pulofesa Mumba.
Popeleka chigamulo chake atamva mbali zonse zokhudzidwa ndi nkhaniyi, Justice Mzondi Mvula, wati mayi Anne adachita zinthu zambiri zodabwitsa zosonyeza kuti ankafuna mamuna wawo asakhale ndi moyo.
Justice Mvula anati zinali zodabwitsa kuti Anne sanagwilitse ntchito galimoto yabanjali kutengera a Mumba ku chipatala atayamba kudwala, m’malo mwake anaimbira foni ambulasi kuti idzawatenge.
Bwaloli lati khalidweli linasonyeza kuti mayi Anne anapanga dala chidodo kuwatengera amuna awo a Mumba ku chipatala kamba koti ankafuna kuti pulofesa Mumba amwalire.
Bwalo la milanduli linatsutsanso zomwe anenena Anne kuti Malemu Mumba ankakana kupita kuchipatala ponena kuti asanamwalire malemuwa akhala akupita ku chipatala pa vuto lomwe anali nalo lakuthamanga kwa magazi.
Bwaloli lati potengera zomwe zinachitika patsiku lainfa ya a Mumba komaso thupi lawo litaikidwa m’manda, nzosakaikitsa kuti mayi Anne ankafuna amunawowa amwalire ndicholinga choti iwo atenge chuma.
Pomaliza bwaloli lakhazikitsa tsiku la 25 July chaka chino ngati lomwe lidzapeleke chilango kwa mayi Anne.