Mabedi amakhumba kuti Sao Tome isachinye olo chimodzi

Advertisement
Patrick Mabedi

Mphunzitsi wa timu ya Mpira wa miyendo wa amuna ya Flames Patrick Mabedi wati linali khumbo lake kuti asachinyitse chigoli ngakhale chimodzi mu masewelo amene anasewera ndi Sao Tome and Principe lachinayi pa bwalo la Bingu mu mzinda wa Lilongwe .

Poyankhula ndi atolankhani atatha masewero olimbilana malo ku masewelo a pa dziko lonse a mchaka cha 2026 (World Cup 2026), Mabedi wati osewera ake amakanika kugwirana miyendo pena zomwe zinapeleka mpata wa chigoli chimodzi kwa Timu ya pa chilumbayi.

Mphunzitsiyu anati kukanika kugwirana miyendo kunadza chifukwa osewerawa sanakhale ndi nthawi yayitali kusewelera limodzi ndipo anati anaphonya mipata ina yomwe samayenera ndipo akonza kuti masewero amene atsala achite bwino kuposela pano.

Mabedi wati nkofunika osewerawa asakhazikike ndi kukondwa kwambiri pa chipambano cha masewelo a Sao Tome amene apambana koma kuti nkofunika kumvetsa za cholinga cha masewelo aliwonse amene asewele mtsogolomu ndipo kuti kupambanaku kungokhala chilimbikitso chabe.

Timu ya Malawi yapambana masewelo ake omwe imasewela ndi Sao Tome and Principe ndi zigoli zitatu kwa chimodzi zomwe anagoletsa ndi Chawanangwa Kawonga, Lanjesi Nkhoma ndi Chifundo Mphasi ndipo anyamata a pa chilumba cha Sao Tome anabweza kudzela kwa Silva.

Malawi yomwe ikhale ikukasewelanso ndi Equatorial Guinea, ili pa nambala ya chitatu mu gulu H ndi ma pointi 6 pamene Tunisia ikutsogolera ndi ma pointi 9 kutsatilana ndi Namibia ndi ma pointi 7, Liberia ili pa nambala yachinayi ndi mapointi 4 pamene Equatorial Guinea ndi Sao Tome alibe pointi iliyonse .

Advertisement