Tithandizeni ndi njira za makono za intaneti – Kunkuyu

Advertisement
Moses Kunkuyu

Nduna yowona za Mauthenga ndi Makina a Digito m’dziko muno a Moses Kunkuyu wapempha dziko la Korea komanso mayiko amuno mu Africa kuti aganizire nkhani yokhudza njira za makono zomwe pachingerezi zimatchedwa kuti Information, Communication and Technology (ICT) ndicholinga chofuna kusintha miyoyo ya anthu amuno mu Africa.

A Kunkuyu amayankhula izi m’dziko la Korea pamkumano wa nachikhumi wotchedwa Global ICT Leadership Forum womwe cholinga chake ndikubweretsa pamodzi akuluakulu a m’dzikolo komanso ochokera m’mayiko amuno mu Africa kuti akambirane pankhani yokhudza kugwilira ntchito limodzi pofuna kupititsa patsogolo chitukuko chokhazikika chomwe pachingerezi ndi Sustainable Development Goals (SDG)

A Kunkuyu ati mpofunika kuti mayiko omwe ali otukuka athandizire mayiko a muno mu Africa kuti nawo atukuke pankhani zokhudza njira za makono za ICT.

Malingana ndi a Kunkuyu ati maiko ambiri amuno mu Africa akukumana ndi mavuto osiyanasiyana kuphatikizapo, nkhani yokhudza kulumikizana, zomangamanga, luso komanso kusatetezeka kwa fiber. 

A Kunkuyu anati ngati izi zitakonzedwa ndiye kuti dziko la Korea komanso mayiko amuno mu Africa zitha kuthandizira kulumikizana mosavuta.

Nayo nduna yowona zasayansi ndi ICT ya mdziko la Korea a Dr. Lee Jong-Ho atsimikizira mayiko amuno mu Africa kuti dzikolo likudzipereka kwa thunthu kugwira ntchito limodzi ndi mayiko amu Africa pa nkhani za ICT.

A Lee Jong-Ho anatinso tonse tikukhala mdziko limodzi kotero iwo sakufuna kuti mayiko amu Africa akhalire pankhani za njira zamakono za ICT paza ulimi komanso maphunziro ndi zina zambiri.

Msonkhanowu unasonkhanitsa mayiko osiyanasiyana amuno mu Africa monga Malawi, Tanzania Eswatini ndi ena ambiri pa mutu oti Kulimbitsa mgwirizano wa Padziko Lonse mu Sophisticated Digital.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.