Chilima akakhala nawo pa mkumano wa ophunzira a Chikatolika ku Sukulu ya Ukachenjede ya Malawi

Advertisement
Saulos Chilima

Wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino, Dr Saulosi Klaus Chilima, akuyembekezeka kudzakhala nawo pa mkumano omwe wakonzedwa ndi ophunzira a Bungwe la Katorika ku Sukulu ya Ukachenjede ya Malawi ku Zomba pa 4 May chaka chino yomwe idzachitike ndi mutu okuti “Call for Evangelisation.”

Wapampando wa Bungweli, Wisdom Sauka, wauzza Malawi24 kuti zochitika patsikuli zidzayamba ndi mwambo wa Missa yomwe adzatsogolere ndi Bishop Alfred Mateyu Chaima wa Diocese ya Zomba.

Sauka watinso ophunzira akale adzakhala nawo pamwambowo ndipo wati ophunzirawa ayitananso wachiwiri kwa m’tsogoleri wadziko lino Dr Chilima ngati mmodzi mwa ophunzira akale apa sukuluyi.

Iye wati cholinga cha mkumanowu ndikufuna kudzakambirana zomavuto omwe ophunzira a bungweli amakumana nawo monga kusowa kwa malo opemphelera monga Tchalichi ndipo iye adapereka chitsanzo choti ophunzira anzawo aku  LUANAR alindi tchalichi pa sukulu yawo momwe amapemphera mosavuta.

“Ife a bungwe la ophunzira a Chikatorika pano pa sukulu ya Ukachenjede ya Malawi takonza mkumanowu ndipo tayitana wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino komanso tayitana ena mwa ophunzira akale omwe adaphunzira pa UNIMA kuti tidzawalongosolere zamavuto omwe timakumana nawo tikafuna kupemphera,” adatero Sauka.

Mwazina zomwe zikuyembekezeka kukachitika patsikuli ndi monga chinkhoswe chongoyeselera, magule amakolo athu komanso zakudya za chi Malawi ndi zakumwa.

Advertisement