Mulili wa chikuku wabuka m’boma la Mchinji

Advertisement
Malawi24

Unduna wa za umoyo wati m’boma la Mchinji mwagwa muliri wa matenda a chikuku omwe pano agwira anthu asanu ndi awiri (7) m’bomali.

Malingana ndi kalata yomwe wasayinira ndi mkulu wa zaumoyo m’bomali, Dr Yohane Mwale, pakadali pano mulili m’mudzi mwa Mtiwa m’dera la Chamveka, mfumu yayikulu Simphasi wachulukira.

Kalatayi ikusonyeza kuti pa 12 April chaka chino, anthu okwana khumi (10) ochokera m’mudzi mwa Mtiwa m’bomali, anaonetsa zizindikiro za matendawa zomwe zinapangitsa kuti ofesi ya zaumoyoyi kuganiza zokawayeza anthuwa.

Ofesi ya zaumoyo m’bomali yati zotsatira za kuchipatala komwe anakayeza anthuwa, zikusonyeza kuti mwa anthu 10 omwe anaonetsa zizindikiro, anthu 7 ndi omwe atsimikizika kuti akudwaladi matendawa.

Ofesiyi yati anthu asanu ndi m’modzi mwa odwalawa ndi ana osapitirira zaka 15 kupatula m’modzi yekha yemwe ndi wa zaka 23.

Pakadali pano, ofesiyi mogwirizana ndi mabungwe osiyanasiyana yakhazikitsa ntchito yolimbana ndi muliriwu yomwe ndi kuphatikizapo kampeni yopereka katemera wa chikuku kwa ana onse osapitirira zaka 15 a m’derali ndi madera ozungulira. Ntchitoyi  ikuyamba pa 30 April, 2024.

Kupatula apo, ofesiyi yati ikhala ikufufuzabe ngati paliso anthu ena omwe akodwa matendawa m’derali komaso madera ozungulira makamaka midzi yonse yomwe ili m’madera a zipatala za Kochilira, Chioshya, Mphelero, Ludzi, Tembwe, Guillime ndi Nkhwazi.

Chikuku ndi matenda omwe amafala mosavuta ndipo amapereka chiopsezo chachikulu pa umoyo wa anthu makamaka kwa ana ndipo zina mwa zizindikiro za matendawa ndi monga; kutentha thupi, chifuwa, chinfine, maso ofiira amisozi, zironda zakukhozi, ndi timatuza tofiira ta pakhungu.

Matendawa amafala kudzera muzinthu za madzimadzi zochokera kwa odwala monga potsokomola, kuyetsemula ndipo munthu amakhala otetezedwa kutenga matendawa pomwe walandira katemara wa chikuku.

Advertisement