Zomwe yachita nduna yakale ya boma la m’gwirizano wa Tonse a Timothy Mtambo podzudzula boma pa mavuto omwe akuta dziko lino zadzidzimutsa akatswiri komanso anthu m’dziko lino.
Pothilira ndemanga pa zomwe a Mtambo anena dzulo pa msonkhano wa atolankhani mu mzinda wa Lilongwe pomwe anati utsogoleri wa pulezident Chakwera walephera kuthetsa mavuto omwe a Malawi akukumana nawo, a Malawi ambiri kudzera m’masamba a m’chezo ati ndi odabwa kuti a Mtambo akunena izi pano pomwe akhala ali chete pa zaka zomwe akhala ali nduna .
Mwa zina, a Mtambo omwenso ndi mtsogoleri wa gulu la ndale Citizen for Transformation (CFT) anapereka chitsanzo cha kukwera mtengo kwa katundu osiyanasiyana, njala, kulephera kupanga ziphaso zoyendera ngati mavuto omwe boma likulephera kuthana nawo.
Koma polemba kudzera pa tsamba la mchezo a Musamuse Vitumbiko ati ndi zovuta kukhulupilira a Mtambo pa zomwe akunenazi kamba iwo akhala ali chete pa zaka zonse zomwe akhala ali nduna.
Kumbali yake omenyala ufulu odziwika bwino m’dziko lino, a Undule Mwakasungula ati a Mtambo amayenera kupereka njira zothanirana ndi mavutowa osati kungodzudzula.
A Mwakasungula ati chiganizo cha a Mtambo povomera kuwasankha kukhala nduna zitha kukhala kuti zinachotsa chikhulupiliro cha a Malawi pa ntchito yawo yomenyera ufulu wa anthu m’dziko lino.
A Mtambo omwe kwambiri anali pa tsogolo kuchititsa zionetsero zofuna kusintha ulamuliro kuchokera ku chipani cha DPP m’chaka cha 2019 atsindika kufunika koti a Malawi adzibwera poyera Kudzudzula boma zinthu zikalakwika