Watulukira mbuyake wa galu: Chakwera wati Amereka ilekeretu zoletsa a Malawi kupita ku dzikolo

Advertisement
Malawi president Lazarus Chakwera

Uja anati menya galu kuti udziwe mbuye wake n’kutheka adalinga izi. Patangotha maola ochepa boma litatafulira boma la Amereka kamba koletsa anthu ena kupita ku dzikolo kamba ka katangale, naye tate wawo Chakwera wayankhulapo. Iye wati boma la Amereka lilekeletu zoletsa a Malawi oganiziridwa katangale kupita mu dzikolo.

Polankhula mu mzinda wa Lilongwe, a Chakwera amene adakhululukira a Uladi Musa omwe nawo adaletsedwa kupita ku dziko la Amereka wati ndi wodabwa ndi chiganizo cha dziko la Amereka.

Iwo ati dziko la Amereka lachita phuma poletsa abambo atatuwa ndi akazi awo ati kamba bwalo la milandu silinawapeze olakwa.

A Chakwera awonjezerapo kuti nalo dziko la Amereka liri ndi zolakwika zambiri zoti ngakhale iwo eni ake sangakonze koma boma la Malawi silichitapo kanthu.

Zokamba za a Chakwera zabwela pamene boma la Amereka lalamula kuti abambo anayi omwe anagwirapo ntchito ndi boma, kuphatikizapo a George Kainja, asazapitenso ku dzikoli.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.