Wakamang’ala ku bwalo Doro wa Zeze: anandinamizira kuti ndinakwera bus pomwe ine ndinakwera ndege

Advertisement
Malawi Dorothy Shonga

Kulitu nkhani ku bwalo uku. A Easter Gondwe omwe amatchuka ndi kukamba nkhani pa tsamba lino la Facebook akasumilidwa. Doro wa Zeze ndiye wakamang’ala kuti a Gondwe ndi a ‘hater’ ndipo amamudyola kwabasi. Akufuna abwalo awalipitse.

Malinga ndi zikalata za ku bwalo zomwe Malawi24 yaona, a Dorothy Shonga amene nawonso amaziti ndi celebrity komanso ati socialite akagwada ku bwalo kuti lilange Mayi Gondwe.

Dorothy Shonga
The Kingstons

Malinga ndi zikalatazi, a Shonga omwe ali pa banja ndi oyimba chamba cha Amapiano Zeze ati Mayi Gondwe akhala akuwanamizira mabodza ofuna kuipitsa mbiri yawo.

“Mwa zina, akhala akuuza anthu kuti ine ndimapanga ma kanema olaula,” atero oyimira milandu Mayi Shonga poulula zina mwa zipongwe zimene a Gondwe akhala akuchita.

“Komanso Mayi Gondwe akhala akufuna kundionetsa ngati ine ndi tambwali, komanso hule,” apitiriza choncho Mayi Shonga kudzera mwa owayimira.

Iwo ati Mayi Gondwe analembapo pa tsamba lawo la Facebook kuti a Shonga adanama zoti adakwera ndege pamene adali nawo limodzi mu bus. Owayimira ati ili ndi bodza lochokera kwa Mayi Gondwe lomwe amangofuna kunyonzetsa Mayi Shonga a Zeze.

Padakali pano Mayi Gondwe alemba motchalenja pa masamba awo a Facebook kuti awapeze ndi zisamani ndipo akaonetsana bwino ku bwalo komweko.

Advertisement