Mudzililire nokha, bweretsani samanizo – wabweza moto Easter Gondwe

Advertisement

Mayi Easter Gondwe omwe akasumilidwa kuti akhala akunyoza nthiti ya oyimba Zeze Kingston, Dorothy, pa fesibuku, ayima pachulu ndikuuza onse omwe akuwavera chisoni kuti adzililire okha ngakhale zikuveka kuti munthu wina wa chiwiri wakawamang’aliraso.

Izi zikudza pomwe Dorothy yemweso amadziwika ndi dzina loti ‘Cash Madam’, wakamang’ala ku bwalo la milandu munzinda wa Lilongwe kuti Gondwe wakhala akumunyalapsya komaso kumuchepsya kudzera pa tsamba la fesibuku.

Cash Madam wakamang’ala ku bwalo la milandu.

Malinga ndi zikalata za ku bwalo la milandu zomwe Malawi24 yaona, mayi Kingstone adandaula kuti mayi Gondwe akhala akuwapekera nkhani zabodza ndikumazithira nsinjiro ndicholinga chofuna kuipitsa mbiri yawo.

“Mwa zina, akhala akuuza anthu kuti ine ndimapanga ma kanema olaula. Komanso Mayi Gondwe akhala akufuna kundionetsa ngati ine ndi tambwali, komanso hule,” yatelo mbali ija ya chisamani cha mayi Kingston

Mayi Kingston apitiliza ndi kufotokoza kuti m’mbuyomu mayi Gondwe analembaposo pa tsamba lawo la fesibuku ku wanena kuti ankanamiza anthu kuti anakwera ndege paulendo wawo opita kunja pamene chilungamo chake chinali choti nkazi wa oyimba chamba cha Amapiano-yu anakwera basi (bus) limodzi ndi mayi Gondwe-wo.

Koma pomwe anthu ambiri amayembekeza kuti mayi Gondwe atseka pakamwa ndi kubunthama, iwo alemba pa tsamba lawo la fesibuku motchalenja komaso mowonetsa kuti aponda mwala.

Iwo anenetsa kuti sakuopa kalikose pa mlandu omwe Dorothy wakawasumira, ponena kuti masiku ano munthu aliyese akumayenda okonzeka kukumana ndi chili chonse.

“Guys stop crying on my behalf (siyani kulira m’malo mwa ine), ma summon bweletsani ndithu.

“Kumaputa anthu pa social media kumati ndikakusumila aliyense amayenda okonzenzeka masiku ano,” ateloso mayi Gondwe m’ma uthenga awiri omwe anawalemba mosiyana.

Mu uthenga wina otsatira pa tsamba lawo lomwelo, mayi Gondwe atiso chisamani chomwe Dorothy anawadulira achibweza  kamba koti chinali ndi zolakwika zina kuphatikizapo dzina lawo.

“Chisamani chinabwela koma ndachibwenza dzina langa ndine Easter not Esther. Tichidikila ndithu,” alembaso choncho mayi Gondwe.

Malipoti ena osatsimikizika omwe akuyenda m’masamba anchezo, akusonyeza kuti munthu winaso otchedwa Frank Banda, wasumiraso mayi Gondwe pa nkhani yomunyoza kudzera pa tsamba la fesibuku.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.