Alimi m’dziko muno awalangiza kuti azibzala mbeu zosiyanasiyana ngati njira imodzi yothana ndi vuto losowa chakudya chokwanira komaso kusintha kwa nyengo.
Mkulu wa Lilongwe District Agriculture Extension Coordinating Committee (DAECC) Akunsitu Kananji ndiye anayankhula izi pa tsiku la alangizi a za ulimi mu mzinda wa Lilongwe ndipo walimbikitsa alimi kubzala mbeu zosiyanasiyana ngati njira imodzi yochulukitsa zokolora komaso phindu la ndalama.
“Masiku ano mvula ikusinthasintha kagwedwe kake, nthawi zina kumakhala chilala kapena mvula ya mphamvu choncho tikufuna alimi asamangodalira chimanga koma azibzalaso mbeu zina zimene zimapilira ku chilala,” iwo anatero.
Mai Judith Khwenja, omwe ndi modzi mwa alimi amene anali nawo pa mwambowu, alimbikitsa alimi anzawo kugwiritsa ntchito malangizo onse amene alangizi a za ulimi amapereka.
Mai khwenja anati “Uwu ndi mwai wathu ife monga alimi amene timalima ngati bizinezi chifukwa kuti mulimi akakolora mbeu zochuluka ndi kugulitsa, apanga mpindu lochulukaso.”
Mkulu wa khonsolo ya Lilongwe, khasala Dan mtayamanja walangiza alimi m’dziko muno kuti asiye kugulitsa mbeu kwa ma venda pa mitengo yosavomerezeka ndi boma